Ndandanda ya Mlungu wa October 28
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 28
Nyimbo Na. 97 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 2 ndime 20-27 ndi bokosi patsamba 29 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Timoteyo 1 -6mpaka 2 Timoteyo 1-4 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: “Kodi Mudzachita Zotani pa Nthawi ya Holide?” Nkhani.
Mph. 10: Thandizani Ena Kuti Aone Phindu la Uthenga Wabwino. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki patsamba 159. Sonyezani mmene tingagwiritsire ntchito nkhani yopezeka m’buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, mogwirizana ndi gawo lanu.
Mph. 15: N’chifukwa Chiyani Kusunga Nthawi N’kofunika? Nkhani yokambirana. (1) Kodi Yehova amasonyeza bwanji chitsanzo chabwino pa nkhani yosunga nthawi? (Hab. 2:3) (2) Kodi timasonyeza bwanji kuti timalemekeza Yehova komanso kuti timaganizira anthu ena tikamapewa kufika mochedwa pa misonkhano komanso polowa mu utumiki? (3) Kodi kagulu ka utumiki wakumunda komanso wochititsa msonkhano wokonzekera utumiki wa kumunda amakhudzidwa bwanji tikafika mochedwa pa msonkhanowu? (4) N’chifukwa chiyani tiyenera kusunga nthawi tikamapita kwa munthu wachidwi amene tinagwirizana naye kapena wophunzira Baibulo wathu? (Mat. 5:37) (5) Kodi ndi malangizo otani amene angatithandize kuti tizisunga nthawi mu utumiki komanso pa misonkhano ya mpingo?
Nyimbo Na. 69 ndi Pemphero