Gwiritsani Ntchito Webusaiti Yathu Pophunzitsa Ana Anu
1. Kodi cholinga cha gawo lakuti “Ana,” lomwe lili pawebusaiti yathu n’chiyani?
1 Webusaiti yathu ya jw.org inakonzedwa m’njira yakuti anthu a misinkhu yonse azisangalala nayo. Mwachitsanzo, pawebusaitiyi pali gawo la mutu wakuti “Ana.” (Pitani pamene alemba kuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa > Ana) Nkhani ndi zinthu zina zimene zili pagawoli zimathandiza ana ang’onoang’ono pamodzi ndi makolo awo kuti azikondana komanso kuti azikonda Yehova. (Deut. 6:6, 7) Kodi mungagwiritse ntchito bwanji zinthu zimene zili pagawo limeneli pophunzitsa ana anu?
2. N’chiyani chingakuthandizeni kusankha zinthu zogwirizana ndi msinkhu wa ana anu zoti muphunzire?
2 Muzisankha Nkhani Zogwirizana ndi Anawo: Mwana aliyense amakhala wosiyana ndi ana ena. (1 Akor. 13:11) Ndiyeno n’chiyani chingakuthandizeni kusankha nkhani zoyenerera zoti muphunzire ndi ana anu? Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndi nkhani zotani zimene anawa angasangalale nazo? Kodi angamvetse zinthu zochuluka bwanji? Pa nthawi iliyonse ndikamaphunzira nawo, kodi tizitenga nthawi yaitali bwanji?’ Mungagwiritse ntchito nkhani zakuti, “Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo.” Mungagwiritsenso ntchito nkhani ndi zinthu zina zimene mungapeze pamagawo otsatirawa a webusaitiyi:
3. Kodi makolo angatani kuti azigwiritsa ntchito moyenera nkhani zimene zili pagawo lakuti “Zochita pa Kulambira kwa Pabanja”
3 Zochita pa Kulambira kwa Pabanja: Zinthu zimene zili pagawo limeneli zingathandize mitu ya mabanja kuphunzitsa ana awo. Dinani kabatani kakuti “Koperani” kuti mukopere ndi kuwerenga “Zothandiza Makolo.” Zimenezi zingakuthandizeni kudziwa malangizo amene mungatsatire pophunzira ndi ana anu. Mungaphunzitse ana ang’onoang’ono pogwiritsa ntchito zithunzi, monga zimene angathe kuzikongoletsa ndi chekeni. Thandizani ana okulirapo kuti achite zimene zili pagawo lakuti “Zoti Muchite Pophunzira.” Zinthu zonse zimene zili pagawo limeneli zimafotokoza nkhani zofanana za m’Baibulo, choncho pa nthawi ya kulambira kwa pabanja, ana a misinkhu yonse angakwanitse kuyankha mafunso amene mungafunse, mogwirizana ndi msinkhu wawo.
4. Kodi pagawo lakuti “Khalani Bwenzi la Yehova” pamapezeka zinthu zotani?
4 Khalani Bwenzi la Yehova: Pagawo limeneli pali mavidiyo, nyimbo ndi zinthu zina zimene zingathandize makolo kukhomereza Mawu a Mulungu m’mitima mwa ana awo ang’onoang’ono. (Deut. 31:12) Mavidiyo afupiafupi a makatuni omwe ali pagawoli angathandize ana kuphunzira zinthu zofunika kwambiri. Palinso zinthu zina zimene zingathandize kwambiri ana kuphunzira zinthu zofunikira m’njira yosangalatsa. Mwachitsanzo, ana angafufuze zinthu zimene zikusowa komanso zimene zalakwika pazithunzi. Nthawi ndi nthawi, pagawoli pamaikidwanso nyimbo za Ufumu komanso nyimbo zina zimene zakonzedwera ana. Popeza ana nthawi zambiri amakonda kuimba, nyimbo zimenezi zimathandiza kwambiri ana kuphunzira komanso kukumbukira zimene aphunzirazo.
5. N’chifukwa chiyani makolo ayenera kupempha Yehova kuti awathandize pophunzitsa ana awo choonadi?
5 Makolo, Yehova akufuna kuti zinthu zizikuyenderani bwino pophunzitsa ana anu. Choncho muzimupempha kuti akuthandizeni pamene mukuphunzitsa ana anu choonadi. (Ower. 13:8) Mothandizidwa ndi Yehova, mungakwanitse kuphunzitsa ana anu kuti akhale ndi ‘nzeru zowathandiza kuti adzapulumuke kudzera m’chikhulupiriro chokhudza Khristu Yesu.’—2 Tim. 3:15; Miy. 4:1-4.