Ndandanda ya Mlungu wa October 21
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 21
Nyimbo Na. 32 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 2 ndime 14-19 ndi bokosi patsamba 25 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Atesalonika 1-5 mpaka 2 Atesalonika 1-3 (Mph. 10)
Na. 1: 1 Atesalonika 2:9-20 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Tingaphunzire Chiyani pa Zinthu Zabwino Komanso Zoipa Zimene Solomo Anachita?—Aroma 15:4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yakuti Zipembedzo Zizichitira Zinthu Limodzi?—rs tsa. 86 ndime 1—tsa. 87 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 15: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Maliko 1:40-42, Maliko 7:32-35 ndi Luka 8:43-48. Kambiranani mmene nkhani zopezeka m’malembawa zingatithandizire pa utumiki wathu.
Mph. 15: “Gwiritsani Ntchito Webusaiti Yathu Pophunzitsa Ana Anu.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Mukamakambirana ndime 3, fotokozani gawo limene limakhala ndi nkhani zakuti “Zothandiza Makolo” ndipo mupereke chitsanzo cha malangizo amene amapezeka pagawo limeneli. Pokambirana ndime 4, pempheni mabanja kuti anene mmene akhala akugwiritsira ntchito webusaiti yathu yovomerezeka pochita kulambira kwa pabanja. Ngakhale m’dera lanu mulibe Intaneti, nkhaniyi ingathandizebe kwambiri makolo. Ngati muli kudera loterolo, ingokambiranani mfundo za m’nkhaniyi zimene mukuona kuti zingakuthandizeni. Limbikitsani makolo kuti azigwiritsa ntchito Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani pofufuza nkhani zimene angaphunzire ndi ana awo pa kulambira kwa pabanja bukuli likadzayamba kupezeka.
Nyimbo Na. 88 ndi Pemphero