Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 October tsamba 2-5
  • 1925—Zaka 100 Zapitazo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 1925—Zaka 100 Zapitazo
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZIMENE TIMAYEMBEKEZERA ZIKALEPHEREKA
  • ANAMANGA NYUMBA ZAMBIRI ZOULUTSIRA MAWU
  • KUMVETSA MFUNDO ZA CHOONADI
  • KUCHITIRA UMBONI ZA YEHOVA
  • KUBWERERA KWA ANTHU AMENE ANASONYEZA CHIDWI
  • ZIMENE ZINADZACHITIKA M’TSOGOLO
  • 1924—Zaka 100 Zapitazo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • 1922​—Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kutumikira ndi Gulu Lopita Patsogolo Koposa
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Njira Zolalikirira​—Ankagwiritsa Ntchito Njira Zosiyanasiyana Kuti Anthu Amve Uthenga
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 October tsamba 2-5
Abale ndi alongo ali panja akujambulitsa chithunzi pamsonkhano wa mu 1925 mumzinda wa Indianapolis, ku Indiana.

Msonkhano wa mumzinda wa Indianapolis ku Indiana mu 1925

1925—Zaka 100 Zapitazo

NSANJA YA OLONDA ya January 1, 1925 inanena kuti, “Akhristu akhala akuyembekezera mwachidwi chaka chimenechi.” Komabe Nsanjayo inanenanso kuti, “Akhristufe sitikuyenera kuda nkhawa kwambiri ndi zimene zichitike m’chaka chimenechi mpaka kufika posiya kugwira mosangalala ntchito imene Ambuye anatipatsa.” Kodi Ophunzira Baibulo ankayembekezera kuti mu 1925 muchitika zotani? Nanga n’chiyani chimene chinawathandiza kuti azigwirabe ntchito yolalikira mwakhama ngakhale kuti zimene ankayembekezera sizinachitike?

ZIMENE TIMAYEMBEKEZERA ZIKALEPHEREKA

Mu 1925 Ophunzira Baibulo ambiri ankayembekezera kuti dzikoli likhala Paradaiso. N’chifukwa chiyani? M’bale Albert Schroeder amene kenako anadzatumikira m’Bungwe Lolamulira ananena kuti: “Tinkakhulupirira kuti mu 1925 odzozedwa adzapita kumwamba ndipo Akhristu okhulupirika monga Abulahamu, Davide ndi ena ambiri adzaukitsidwa n’kumatsogolera anthu padzikoli monga akalonga a Ufumu wa Mulungu.” Komabe abale ndi alongo ena anakhumudwa ataona kuti chakachi chikupita kumapeto koma zimene amayembekezera sizikuchitika.—Miy. 13:12.

Ngakhale kuti anakhumudwa, Ophunzira Baibulo ambiri anapitirizabe kulalikira mwakhama. Iwo anayamba kuzindikira kuti kulalikira zokhudza Yehova inali ntchito yofunika kwambiri. Mwachitsanzo, tiyeni tione zimene anachita kuti alalikire anthu ambiri pogwiritsa ntchito wailesi.

ANAMANGA NYUMBA ZAMBIRI ZOULUTSIRA MAWU

Mu 1924 anthu ambiri anamvetsera wailesi ya WBBR. Izi zinachititsa kuti mu 1925, Ophunzira Baibulo amange nyumba ina yamphamvu kwambiri youlutsira mawu ndipo pa nthawiyi anaimanga pafupi ndi mzinda wa Chicago ku Illinois. Nyumbayi inkadziwika ndi dzina lakuti WORD. Ralph Leffler yemwe ndi katswiri amene anagwira ntchito yomanga nyumbayi ananena kuti “m’nyengo yozizira madzulo anthu a m’madera ambiri akutali ankamvetsera nawo wailesiyi.” Mwachitsanzo, banja lina limene linkakhala pamtunda woposa makilomita 5,000 mumzinda wa Pilot Station ku Alaska linamvetsera nawo imodzi mwa nkhani zoyambirira kuulutsidwa. Pambuyo pomvetsera, banjali linalemba kalata kwa anthu amene ankagwira ntchito ku wailesiyi yowathokoza chifukwa cha pulogalamu yauzimu yolimbikitsa.

Kumanzere: Matawa a nyumba youlutsira mawu ya WORD ku Batavia ku Illinois

Kumanja: Ralph Leffler akugwira ntchito m’nyumba youlutsira mawu

Nsanja ya Olonda ya December 1, 1925 inafotokoza chifukwa chake anthu a m’madera akutali kwambiri ankakwanitsa kumvetsera wailesiyi, inanena kuti: “Wailesiyi ndi imodzi mwa mawailesi amphamvu kwambiri m’dziko la United States. Anthu amene akukhala m’mbali mwa nyanja kum’mawa ndi kumadzulo kwa United States, Cuba komanso kumpoto kwenikweni kwa Alaska akutha kumvetsera wailesiyi. Wailesiyi ikuthandiza anthu amene anali asanamvepo choonadi kukhala ndi chidwi chofuna kumva zambiri.”

George Naish

Pa nthawi imeneyinso Ophunzira Baibulo anakonza zoti azigwiritsa ntchito wailesi polalikira uthenga wabwino ku Canada. Mu 1924 anamanga nyumba youlutsira mawu yotchedwa CHUC ku Saskatoon ku Saskatchewan. Nyumbayi inali imodzi mwa nyumba zachipembedzo zoyambirira zoulutsira mawu ku Canada. Mu 1925, anasamutsira nyumba youlutsira mawuyi ku malo ena aakulu. Choncho bungwe la Watch Tower Society linagula nyumba yakale ya Regent Building yomwe ankachitiramo masewera ku Saskatoon, n’kuikonza kuti aziulutsiramo mawu ndipo anasamutsira masitudiyo awo m’nyumbayi.

Wailesi ya CHUC inathandiza anthu ambiri amene ankakhala m’matauni ang’onoang’ono komanso m’madera akumudzi a ku Saskatchewan kuti amve uthenga wabwino kwa nthawi yoyamba. Mwachitsanzo, m’tauni ina yakutali, Mayi Graham atamvetsera wailesiyi analemba kalata yopempha mabuku othandiza pophunzira Baibulo. M’bale George Naish ananena kuti, “Pempho la mayiyu linali loonekeratu kuti ankafunitsitsa kuyamba kuphunzira mwamsanga moti tinamutumizira buku la Studies in the Scriptures.” Pasanapite nthawi, Mayi Graham anayamba kulalikira uthenga wa Ufumu m’madera akutali kwambiri.

KUMVETSA MFUNDO ZA CHOONADI

Nsanja ya Olonda ya March 1, 1925 inali ndi mutu wosaiwalika wakuti “Kubadwa kwa Mtundu.” N’chifukwa chiyani nkhani imeneyi inali yofunika? Ophunzira Baibulo ankadziwa kuti Satana ali ndi gulu lomwe ndi lopangidwa ndi angelo oipa omwe ndi osaoneka ndipo amatsogolera magulu azipembedzo, amalonda komanso andale padzikoli. Komabe pogwiritsa ntchito nkhaniyi “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” anathandiza abale kuzindikira kuti nayenso Yehova ali ndi gulu lake, lomwe ndi losiyana kwambiri ndi gulu la Satana ndipo limatsutsa zochita za gulu la Satana. (Mat. 24:45) Kuwonjezera pamenepa, kapoloyu anafotokozanso kuti Ufumu wa Mulungu unali utayamba kulamulira mu 1914. Chaka chomwechi ndi chimenenso kumwamba kunachitika nkhondo ndipo zotsatira zake Satana ndi ziwanda zake anathamangitsidwa kumwambako moti panopa ali padziko lapansi pano.—Chiv. 12:​7-9.

Ophunzira Baibulo ena zinkawavuta kumvetsa mfundo yatsopanoyi. Poganizira zimenezi Nsanjayi inanena kuti: “Ngati pali ena amene sakuvomereza zimene zafotokozedwa munkhaniyi, tikuwapempha kuti apitirize kudikira Ambuye moleza mtima, n’kumapitirizabe kumutumikira mokhulupirika.”

Tom Eyre wa ku Britain yemwe anali kopotala (panopa timanena kuti apainiya) anafotokoza mmene nkhaniyi inakhudzira Ophunzira Baibulo ambiri. Iye anati: “Abale anasangalala ndi mmene nkhaniyi inafotokozera buku la Chivumbulutso chaputala 12. Titazindikira kuti Ufumu wakhazikitsidwa kumwamba tinasangalala kwambiri ndipo tinkafunitsitsa kuuza ena za uthenga wabwinowu. Inatilimbikitsa kuti tizifuna kuchita zambiri pa ntchito yolalikira komanso inatithandiza kudziwa kuti Yehova akutsogolera gulu lake kuti lidzakwanitse kuchita zazikulu m’tsogolo.”

KUCHITIRA UMBONI ZA YEHOVA

Masiku ano, a Mboni za Yehova amadziwa bwino mawu a pa Yesaya 43:10 akuti: “‘Inu ndinu mboni zanga,’ akutero Yehova, ‘Inde, mtumiki wanga amene ndamusankha.’” Komabe chaka cha 1925 chisanafike lemba limeneli silinkagwiritsidwa ntchito kwambiri m’mabuku athu. Koma zinthu zinali zitatsala pang’ono kusintha. Mu 1925, Nsanja ya Olonda inagwiritsa ntchito lemba la Yesaya 43:10 ndi 12 munkhani 11 za m’magazini athu.

Kumapeto kwa August mu 1925, Ophunzira Baibulo anachita msonkhano wachigawo mumzinda wa Indianapolis ku Indiana. Papulogalamu ya msonkhanowo M’bale Joseph F. Rutherford analembapo mawu olandirira alendo akuti: “Tabwera pamsonkhanowu kuti tipeze . . . mphamvu kuchokera kwa Ambuye n’cholinga choti tikabwerera tikapitirize kugwira ntchito yolalikira mwakhama.” Pamsonkhanowu womwe unachitika kwa masiku 8, anthu analimbikitsidwa kuti azigwiritsa ntchito mpata uliwonse kuchitira umboni za Yehova.

Loweruka pa 29 August M’bale Rutherford anakamba nkhani ya mutu wakuti “Kugwira Ntchito Mwakhama.” Munkhaniyi anatsindika kufunika kogwira ntchito yolalikira. Iye anati: “Yehova akuuza anthu ake kuti . . . : ‘Inu ndinu mboni zanga . . . ndipo ine ndine Mulungu.’ Kenako anawalamula ndi mawu amphamvu akuti, ‘Anthu a mitundu yosiyanasiyana muwakwezere chizindikiro.’ Palibenso anthu ena padziko lapansi amene akukwezera anthu ena chizindikiro kupatulapo [anthu ake], omwe ali ndi mzimu wa Ambuye ndipo ndi mboni zake.”—Yes. 43:12; 62:10.

Kapepala komwe kanali ndi chigamulo chakuti “Uthenga wa Chiyembekezo.”

Kapepala ka Uthenga wa Chiyembekezo

M’bale Rutherford atamaliza kukamba nkhani yake anawerenga chigamulo cha mutu wakuti “Uthenga wa Chiyembekezo.” Abale ndi alongo anagwirizana ndi chigamulocho chomwe chinkanena kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungathe kupangitsa kuti “zinthu ziyambe kuyenda bwino, kubweretsa madalitso amtendere, moyo wabwino, ufulu komanso chisangalalo chosatha.” Patapita nthawi chigamulocho chinamasuliridwa m’zilankhulo zosiyanasiyana n’kupulintidwa patimapepala ndipo anagawira kwa anthu timapepala pafupifupi 40 miliyoni.

Kwa zaka zambiri Ophunzira Baibulo anali asanasinthe dzina kuti ayambe kugwiritsa ntchito dzina lakuti Mboni za Yehova. Komabe iwo anayamba kuzindikira kuti ali ndi udindo wolalikira za dzina la Yehova.

KUBWERERA KWA ANTHU AMENE ANASONYEZA CHIDWI

Pamene chiwerengero cha Ophunzira Baibulo chinkapitiriza kuwonjezereka padziko lonse, gulu la Yehova linkalimbikitsa abale kuti m’malo momangogawira mabuku ayenera kupitanso kwa anthu amene anasonyeza chidwi atamva uthenga wabwino. Pambuyo pa ntchito yapadera yogawira kapepala kakuti Uthenga wa Chiyembekezo, Utumiki wa Ufumua unanena kuti: “Konzani zoti mubwererenso kunyumba zimene simunasiyeko mabuku koma munasiya kapepala ka Uthenga wa Chiyembekezo.”

Nkhani ya mu Utumiki wa Ufumu wa January 1925, inali ndi lipoti limene wophunzira Baibulo wina ku Plano mumzinda wa Texas anapereka. Iye ananena kuti: “Tinachita chidwi kuona kuti m’magawo amene tinalalikiramo maulendo ambiri, anthu ake ankachita chidwi kuposa anthu a m’magawo atsopano. Pa zaka 10 zapitazi takhala tikulalikira m’tauni ina yaing’ono m’gawo lathu kwa maulendo 5. . . . Posachedwapa Mlongo Hendrix limodzi ndi mayi anga anakalalikiranso m’tauniyi ndipo anagawira mabuku ambiri kuposa amene tinagawirapo m’mbuyomu.”

M’dziko la Panama, kopotala wina anati: “Anthu ambiri amene poyamba ankandithamangitsa panyumba zawo ankasintha maganizo ndikawayenderanso kachiwiri kapena kachitatu. Chaka chathachi ndinakonza zoti ndizibwereranso kwa anthu amene ndinawalalikirapo m’mbuyomo ndipo zotsatira zake zinali zabwino kwambiri.”

ZIMENE ZINADZACHITIKA M’TSOGOLO

M’kalata yake yapachaka yopita kwa akopotala onse, M’bale Rutherford anafotokoza zomwe zinachitika m’chaka chimenecho komanso zomwe zinkayenera kuchitika m’tsogolo. Iye anati: “M’chaka chapitachi munali ndi mwayi wolimbikitsa anthu amene anali okhumudwa komanso ankhawa. Ntchito imeneyi yakuthandizani kuti muzisangalala . . . M’chaka chikubwerachi mukhala ndi mwayi wochitira umboni za Mulungu ndi Ufumu wake komanso kusonyeza kuti ndinu olambira ake enieni. . . . Tiyeni tonse tipitirize kufuula mokweza poimba ndi kutamanda Mulungu komanso Mfumu yathu.”

Pamene chaka cha 1925 chinkapita kumapeto, abale anakonza zoti awonjezere nyumba zina ku Beteli ya ku Brooklyn. Ndipo m’chaka cha 1926 munayambika ntchito yaikulu yomanga imene inali isanachitikepo m’gulu la Yehova.

Malo amene abale angoyambapo kumene kugwira ntchito yomanga.

Ntchito yomanga ku Adams Street ku Brooklyn, New York, 1926

a Panopa timati Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena