Achikulire—Ndinu Ofunika Kwambiri Mumpingo
“Ndikayang’ana kumbuyo ndimadabwa ndi zinthu zimene ndinkakwanitsa kuchita. Popeza tsopano ndine wachikulire, sindingakwanitse kuchita zambiri ngati kale.”—Connie, wazaka 83.
Mwina inunso simukutha kuchita zambiri chifukwa cha uchikulire. Ngakhale kuti mwatumikira Yehova kwa zaka zambiri, mukhoza kumadziona ngati wosafunika chifukwa chakuti panopa simungathe kuchita zambiri. Mwachitsanzo, mwina mukhoza kumayerekezera zimene mukuchita panopa ndi zimene munkachita m’mbuyo. Ngati ndi choncho, kodi mungatani kuti muthetse maganizo amenewa?
ZIMENE YEHOVA AMAFUNA KUTI MUZICHITA
Dzifunseni kuti, ‘Kodi Yehova amafuna kuti ndizichita chiyani?’ Mungapeze yankho pa lemba la Deuteronomo 6:5 limene limati: “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse.”
Mogwirizana ndi vesili, Yehova amafuna kuti muzimutumikira ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse. Mfundo imeneyi ingakuthandizeni kuti mupewe kudziyerekezera ndi anthu ena komanso kuyerekezera zimene mukuchita panopa ndi zimene munkachita m’mbuyo.
Taganizira izi: Muli wachinyamata, kodi munkamupatsa chiyani Yehova? Atumiki ambiri a Yehova angayankhe kuti ankamupatsa zonse zimene akanatha. Pa nthawiyo ndi zimene munkakwanitsa kumupatsa malinga ndi mmene zinthu zinalili. Komano kodi panopa mukukwanitsa kumupatsa chiyani Yehova? N’zosachita kufunsa kuti mukumupatsa zonse zimene mungakwanitse mogwirizana ndi mmene zinthu zili pa moyo wanu panopa. Ngati mungaone zinthu mwanjira imeneyi, mukhoza kuona kuti mukupatsa Yehova zonse zomwe mungathe ngati mmene munkachitira m’mbuyo. Kale munkamupatsa zonse zomwe mukanatha, ndipo n’zomwe mukuchitanso panopa.
Pa nthawi imene munali wachinyamata, munkamupatsa Yehova zonse zomwe mukanatha ndipo ndi zomwenso mukuchita panopa pamene muli achikulire
MUKHOZA KUTHANDIZA KWAMBIRI ANTHU ENA
Mfundo ina yofunika ndi iyi: M’malo moona kuti kukhala wachikulire kukulepheretsani kuchita zambiri, muziona kuti kukupatsani mwayi wochita zambiri. Monga Mkhristu wachikulire, panopa mungathe kuchita zinthu zina zimene simukanatha kuchita pamene munali wachinyamata. Mwachitsanzo, mungachite zotsatirazi:
Muzifotokozera ena zimene mwakumana nazo pa moyo wanu. Taonani zimene Baibulo limanena pa mavesi otsatirawa:
Mfumu Davide: “Ndinali mwana ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha chakudya.”—Sal. 37:25.
Yoswa: “Tsopano ine ndatsala pangʼono kufa. Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti palibe mawu ngakhale amodzi pa malonjezo onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena, omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe.”—Yos. 23:14.
Mwina inunso munanenapo mawu ngati amenewa. Davide ndi Yoswa, nawonso anafotokoza zimene zinawachitikira pa moyo wawo. Atumiki a Yehova okhulupirikawa anafotokoza zinthu zimene anaona zikuchitika komanso kumva kwa zaka zambiri, choncho zimene ananena zinali zothandiza kwambiri.
Ngati mwatumikira Yehova kwa nthawi yaitali, inunso mungathe kufotokoza zimene Yehova wakuchitirani komanso kuchitira anthu ena. Kodi mukukumbukira nthawi ina pamene munaona Yehova akuthandiza anthu ake m’njira yapadera kwambiri? Ngati ndi choncho muzifotokozera anthu ena. Zimenezo zikhoza kulimbikitsa abale ndi alongo ngati mmene zinakulimbikitsirani inuyo. Mukamauza anthu ena zimene mwakumana nazo potumikira Yehova mukhoza kuwalimbikitsa kwambiri.—Aroma 1:11, 12.
Njira ina imene mungalimbikitsire ena ndi kupezeka pamisonkhano pamasom’pamaso ngati mungakwanitse kutero. Kumisonkhanoko mungalimbikitse ena komanso inuyo mungalimbikitsidwe. Connie amene tamutchula kale uja ananena kuti: “Kupezeka pamisonkhano kumandithandiza kuti ndisafooke. Ndikapita ku Nyumba ya Ufumu abale ndi alongo amandisonyeza chikondi moti sindidandaula chilichonse. Ndimayesetsa kuwapatsa mphatso posonyeza kuwayamikira ndipo ndimaonetsetsa kuti ndizichita nawo limodzi zinthu zokhudza kulambira.”
YEHOVA AMAYAMIKIRA ZIMENE MUMACHITA POMUTUMIKIRA
M’Baibulo muli nkhani za anthu amene Yehova ankawakonda ngakhale kuti sankachita zambiri chifukwa cha mmene zinthu zinalili pa moyo wawo. Chitsanzo ndi Simiyoni amene anali bambo wachikulire wa Chiisiraeli yemwe anali ndi moyo pamene Yesu anabadwa. Simiyoni akapita ku kachisi ayenera kuti ankaona achinyamata akugwira ntchito zofunika kwambiri. Ndiye kodi Simiyoni ankamva bwanji? N’kutheka kuti ankadziona kuti ndi wosafunika kwa Yehova chifukwa sakanakwanitsa kugwira ntchito ngati achinyamatawo. Koma si mmene Yehova ankamuonera. Iye ankaona kuti Simiyoni “anali wolungama komanso wodzipereka” ndipo anamupatsa mwayi woti aone Yesu ali wakhanda. Yehova anagwiritsanso ntchito Simiyoni kuti anene ulosi wokhudza mwanayu woti adzakhala Mesiya. (Luka 2:25-35) Apatu n’zoonekeratu kuti si kuti Yehova ankangoona kuti Simiyoni ndi wachikulire koma ankaona kuti ndi munthu wachikhulupiriro cholimba “ndipo mzimu woyera unali pa iye.”
Yehova anamupatsa Simiyoni mwayi woti aone Yesu ali wakhanda komanso anene ulosi wokhudza mwanayu kuti adzakhala Mesiya
Inunso musamakayikire kuti Yehova amayamikira zimene mumachita pomutumikira mokhulupirika ngakhale kuti simungakwanitse kuchita zambiri. Yehova amafuna kuti munthu azipereka nsembe “zimene angakwanitse, osati zimene sangakwanitse.”—2 Akor. 8:12.
Choncho muziganizira kwambiri zimene mungakwanitse kuchita. Mwachitsanzo, mungaganizire mitundu ya ulaliki imene mungakwanitse kuchita nawo ngakhale mutachita kwa nthawi yochepa. Mukhozanso kuthandiza ena powaimbira foni mwachidule kapena kuwalembera khadi. Zinthu zing’onozing’ono zosonyeza chikondi zimalimbikitsa kwambiri anthu ena, makamaka zikachokera kwa anthu amene atumikira Yehova kwa nthawi yayitali.
Ena sangachite zambiri chifukwa cha mavuto athanzi. Taonani zimene zinachitikira mlongo wina wa ku East Africa m’bokosi lakuti “Zinapulumutsa Moyo Wake.”
Muzikumbukira kuti kukhulupirika kwanu kukhoza kulimbikitsa anthu ena. Ndinu chitsanzo chabwino pa nkhani yopirira ndipo musamakayikire kuti, “Mulungu si wosalungama kuti angaiwale ntchito yanu ndiponso chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake, potumikira oyera ndipo mukupitiriza kuwatumikira.”—Aheb. 6:10.
MUZITANGANIDWA NDI KUTHANDIZA ENA
Kafukufuku amasonyeza kuti achikulire ambiri omwe amatanganidwa ndi kuthandiza anthu ena amakhala ndi thanzi labwino, amaganiza bwino komanso amakhala ndi moyo wautali.
N’zoona kuti kuchitira ena zabwino sikungachotse mavuto onse amene amabwera chifukwa cha uchikulire. Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse chimene chimayambitsa ukalamba ndi imfa, womwe ndi uchimo umene tinatengera kwa Adamu.—Aroma 5:12.
Komabe utumiki umene mukuchitira Yehova womwe ukuphatikizapo kuthandiza anthu kuti amudziwe, umakuthandizani kuti mupitirize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso thanzi labwino. Achikulire, dziwani kuti Yehova amayamikira zonse zimene mumachita pomutumikira komanso abale ndi alongo mumpingo amayamikira chitsanzo chanu chabwino cha kukhulupirika.