MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA
Muziyerekezera Kuti Mukuona Zomwe Zikuchitika Mukamawerenga Nkhani za M’Baibulo
M’Baibulo muli nkhani za mbiri yakale zomwe zimatiphunzitsa mfundo zofunika. Tikamayerekezera kuti tikuona nkhanizi m’maganizo mwathu, tikhoza kumvetsa bwino zimene tikuwerenga ndipo zikhoza kutithandiza kwambiri. Taonani mfundo zina zomwe zingakuthandizeni kuyerekezera kuti mukuona m’maganizo mwanu nkhani za m’Baibulo.
Muziwerenga mokweza. Kuwerenga Baibulo mokweza kungakuthandizeni kuti muziona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika munkhaniyo. Mukamawerenga Baibulo limodzi ndi banja lanu, aliyense mungamupatse mbali ya winawake wotchulidwa munkhaniyo kuti awerenge ndipo zingakuthandizeni kuti muziona ngati nkhaniyo ikuchitikira inuyo.
Muziona m’maganizo zimene zikuchitika. Muziyesetsa kumvetsa zimene otchulidwa munkhaniyo ankaganiza komanso mmene ankamvera. Mwachitsanzo, muzidzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani munthuyu analankhula komanso kuchita zimenezi? Kodi ineyo bwenzi ndikuganiza kapena kumva bwanji ndikanakhala kuti ndakumana ndi zimenezi?’
Muzijambula zithunzi. Kujambula zimene mukuwerenga m’Baibulo kungakuthandizeni kuti musamavutike kuona zochitikazo m’maganizo komanso kuzikumbukira, ngakhale zitakhala kuti zithunzizo simunazijambule mwaluso kwenikweni.