MBILI YANGA
Kucita Zimene Yehova Watilamula Kumabweletsa Madalitso
“Tidzapita ise!” Umu ni mmene ine, mwamuna wanga, mlongosi wanga na mkazi wake, tinayankhila pamene tinapemphedwa kuti tikacite utumiki winawake. N’cifukwa ciani tinavomeleza utumikiwo? Nanga Yehova anatidalitsa bwanji? Coyamba, lekani n’kuuzeni mmene umoyo wanga unalili poyamba.
N’NABADWILA m’tauni ya Hemsworth mu 1923, ku Yorkshire, m’dziko la England. N’nali na mlongosi mmodzi cabe, dzina lake Bob. N’tafika pafupi-fupi zaka 9, atate, amene anali kudana na cinyengo ca m’machechi, anapeza mabuku ovumbula cipembedzo conama. Iwo anakondwela ngako na zimene anaŵelenga m’mabukuwo. Patapita zaka zocepa, a Bob Atkinson anafika panyumba pathu, ndipo anatenga galamafoni yawo n’kutilizila imodzi mwa nkhani zojambulidwa za M’bale Rutherford. Pamenepo, tinazindikila kuti gulu limene linakonza nkhaniyo n’limenenso linafalitsa mabukuwo. Conco, makolo anga anapempha M’bale Atkinson kuti tsiku lililonse azibwela kunyumba kwathu kudzadya nase cakudya camadzulo, na kudzayankha mafunso ambili a m’Baibo amene tinali nawo. M’bale Atkinson anatipempha kuti tizipezeka ku misonkhano imene inali kucitikila kunyumba kwa M’bale wina, kutali pang’ono na kwathu. Ise sitinazengeleze. Ndipo mpingo waung’ono unakhazikitsidwa ku Hemsworth. Posakhalitsa, tinayamba kulandila atumiki amadela (amene lomba timati oyang’anila dela) kunyumba kwathu. Tinalinso kuitana apainiya apafupi kuti adzadye nase cakudya. Kuceza nawo mwanjila imeneyo kunanilimbikitsa ngako.
Tinafuna kuyamba kucita bizinesi, koma Atate anauza mlongosi wanga kuti, “Ngati ufuna, ungapite kukacita upainiya, ndipo izi tidzazileka.” Bob anavomeleza, ndipo anacoka panyumba kukacita upainiya ali na zaka 21. Pambuyo pa zaka ziŵili, n’naikiwa kukhala mpainiya. Panthawiyo, n’nali na zaka 16. Nthawi zambili n’nali kulalikila nekha, kupatulako kumapeto kwa wiki. N’nali kuseŵenzetsa makadi aulaliki na galamafoni. Koma Yehova ananidalitsa mwa kunithandiza kupeza wophunzila Baibo amene anapita patsogolo mwamsanga. M’kupita kwa nthawi, ambili m’banja la munthuyo anaphunzila coonadi. Caka cotsatila, ine na mlongo Mary Henshall tinaikiwa kukhala apainiya apadela. Tinatumiziwa ku gawo limene kunalibe ofalitsa, m’dela lochedwa Cheshire.
Mkati mwa Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse, akazi analamulidwa kuti azigwilako nchito yocilikiza nkhondo. Pokhala atumiki a nthawi zonse, ise apainiya apadela tinali kuyembekezela kuti boma lidzatipatsa ufulu wakuti tisamagwileko nchito yocilikiza nkhondo, molingana ndi atumiki a machechi ena. Koma makhoti anakana, ndipo ine n’naweluzidwa kuti nikakhale m’ndende masiku 31. Caka cotsatila pamene n’nakwanitsa zaka 19, n’nakalembetsa monga munthu wokana kugwila nchito yocilikiza nkhondo cifukwa ca cikumbumtima cake. Mwa ici, akulu-akulu a boma ananipeleka ku khoti kaŵili konse, koma mlandu unatuluka washauti. Pa zocitika zonsezi, n’nadziŵa kuti mzimu woyela unali kunithandiza, ndi kuti Yehova ananigwila dzanja na kunilimbitsa.—Yes. 41:10, 13.
MNZANGA WATSOPANO
Ine na Arthur Matthews tinadziŵana mu 1946. Iye anakhala m’ndende miyezi itatu kaamba ka cikumbumtima cake pa nkhani yoloŵa usilikali. Atacoka ku jele, anapita ku Hemsworth kukatumikila pamodzi na mng’ono wake Dennis, amene anali mpainiya wapadela. Iwo anaphunzitsidwa za Yehova na atate awo kuyambila ali ana, ndipo anabatizika ali acicepele. Patapita nthawi yocepa, Dennis anatumiziwa ku Ireland. Conco, Arthur anatsala yekha. Makolo anga anacita cidwi na khalidwe la mpainiya wacicepele wodzipeleka ameneyu, cakuti anam’pempha kuti azikhala nawo. Nikapita kukaona anthu kunyumba, ine na Arthur tinali kutsukila pamodzi mbale tikatsiliza kudya. M’kupita kwa nthawi, tinayamba kulembelana makalata. Mu 1948, Arthur anaweluzidwanso kuti akapike ndende miyezi itatu. Mu January 1949, tinakwatilana. Tinali na colinga copitiliza kucita upainiya kwa nthawi yaitali mmene tikanathela. Tikakhala pa chuti, tinali kucita pisiweki yothyola zipatso kuti tizipezako ndalama. Mwa dalitso la Yehova ndiponso cifukwa coseŵenzetsa mwanzelu ndalamazo, tinakwanitsa kupitiliza kucita upainiya.
Mu 1949, ku Hemsworth, titangokwatilana kumene
Patapita caka cimodzi cabe, tinapemphedwa kuti tikatumikile ku Northern Ireland. Poyamba, tinali kutumikila m’tauni ya Armagh, kenako tinakatumikila m’tauni ya Newry. M’matauni amenewa munali kukhala Akatolika ambili. Kunali citsutso coopsa, ndipo tinali kukhala osamala ndi ozindikila pokamba na anthu. Misonkhano inali kucitikila ku nyumba ya m’bale wina, imene inali pamtunda wa makilomita 16 kucokela pamene tinali kukhala. Tinali kusonkhana anthu 8. Akatipempha kuti tigone kumeneko, tinali kugona pansi. M’maŵa, tinali kudya cakudya cogwila pamimba. N’zokondweletsa ngako kuti tsopano m’delali muli Mboni zambili.
“TIDZAPITA ISE!”
Mlongosi wanga na mkazi wake, Lottie, anali kale ku Northern Ireland, kumene anali kutumikila monga apainiya apadela. Mu 1952, tonse anayi tinacitila pamodzi msonkhano wacigawo ku Belfast. M’bale wina anatipatsa malo ogona tonse, kuphatikizapo m’bale Pryce Hughes, amene panthawiyo anali mtumiki wa nthambi ku Britain. Tsiku lina madzulo, tinakambilana za kutulutsiwa kwa kabuku kakuti God’s Way Is Love, kamene anakakonzela maka-maka anthu a ku Ireland. M’bale Hughes anatifotokozela mavuto amene abale anali kukumana nawo polalikila Akatolika m’dziko la Irish Republic. Magulu aciwawa otunthiwa ndi ansembe anali kucotsa abale m’nyumba zawo na kuwacitila nkhanza zosiyana-siyana. M’bale Hughes anati: “Tifuna anthu amene ali na mamotoka kuti akagwile nchito yapadela yogaŵila tumabuku tumenetu m’dzikolo.”a Mwamsanga, tinayankha kuti “Tidzapita ise!” monga n’nakambila kumayambililo kwa nkhaniyi.
Pamodzi na apainiya anzanga pa honda yakangolo kumbali
Kwina kumene apainiya nthawi zambili anali kufikila akapita ku Dublin, kunali kunyumba kwa Ma Rutland, mlongo wokhulupilika amene anali ciyambakale m’coonadi. Ifenso tinafikila kumeneko. Ndipo pambuyo pogulitsa katundu wina amene tinali naye, tonse anayi tinakwela honda ya Bob yakangolo kumbali pokasakila motoka yogula. Tinapeza motoka yakale koma yabwino. Popeza kuti tonse sitinali kudziŵa kuyendetsa, tinapempha amene anatigulitsa kuti atibweletsele motokayo. Pa tsikulo, Arthur, anagona mocedwa cifukwa coganizila za mmene adzayendetsela motokayo. M’maŵa mwake pamene iye anali kufuna kutulutsa motokayo m’galaji, m’mishonale wina dzina lake Mildred Willett, (amene pambuyo pake anakhala mkazi wa John Barr), anafika. Iye anali kudziŵa kuyendetsa motoka. Conco, anatiphunzitsa kuyendetsa, cakuti pambuyo pake tinali okonzeka kuyenda ulendo wathu.
Motoka na kalavani yathu
Ndiyeno, tinayamba kusakila nyumba. Ena anaticenjeza kuti tizipewa kugona m’makalavani kuopela kuti otsutsa angatitenthele mmenemo. Conco, tinafunafuna nyumba yokhalamo koma sitinaipeze cakuti usikuwo tonse tinagona m’motoka. Tsiku lotsatila, pambuyo pofunafuna, tinangopeza cabe kalavani yokhala na mabedi aŵili. Imeneyo ndiyo inakhala nyumba yathu. Cokondweletsa n’cakuti alimi anali kutikomela mtima potilola kuika kalavani yathu pafamu pawo. Tinali kulalikila m’gawo limene linali pamsenga wa makilomita 16 mpaka 24, kucokela pamene tinaika kalavani yathu. Tikakukila kudela lina, tinali kucita maulendo obwelelako kudela kumene tinaikako kalavani yathu poyamba.
Tinalalikila nyumba zonse za kum’mwela ca kum’mawa kwa Irish Republic, popanda covuta ciliconse. Tinagaŵila tumabuku topitilila pa 20,000, ndipo maina a anthu ofuna kuphunzila coonadi tinawatumiza ku ofesi ya nthambi ya Britain. Pano tikamba, kudela limeneli kuli Mboni zambili.
TINABWELELA KU ENGLAND, KENAKO TINAPITA KU SCOTLAND
M’kupita kwa nthawi, tinauzidwa kuti tikatumikile kum’mwela kwa London. Patangopita mawiki ocepa, Arthur analandila foni yocoka ku ofesi ya nthambi ya Britain, yom’pempha kuti adzayambe kugwila nchito ya m’dela tsiku lotsatila. Pambuyo pophunzitsidwa za nchitoyi kwa wiki imodzi, tinapita ku Scotland kukatumikila m’dela limene anatigaŵila. Arthur analibe nthawi yokwanila yokonzekela nkhani zake. Koma mtima wake wodzipeleka kucita nchito zovuta potumikila Yehova, unali kunilimbikitsa ngako. Kukamba zoona, tinali kukondwela maningi m’nchito yadela. Kwa zaka ndithu, tinali kutumikila m’gawo lopanda ofalitsa, koma tsopano tinali na mwayi wotumikila pamodzi ndi abale na alongo ambili-mbili.
Arthur analandila kalata yomuuza kuti akaloŵe Sukulu ya Giliyadi ya miyezi 10 mu 1962. Panthawiyo, tinafunika kupanga cosankha cacikulu. Koma tinaona kuti Arthur anayenela kupita ndithu kusukulu olo kuti zimenezo zikanacititsa kuti ine nikhale nekha. Popeza n’nakhala nekha, ofesi ya nthambi inanitumizanso ku Hemsworth kuti nikatumikile monga mpainiya wapadela. Patapita caka cimodzi, Arthur anabwela, ndipo anaikidwa kukhala woyang’anila cigawo, cimene cinaphatikizapo Scotland, kumpoto kwa England, ndi Northern Ireland.
UTUMIKI WATSOPANO KU IRELAND
Mu 1964, Arthur analandila utumiki watsopano, wokhala mtumiki wa nthambi ku Irish Republic. Tinali kusangalala ngako na nchito yoyendela cigawo. Conco, pamene tinalandila utumiki watsopanowu, n’nakhala na nkhawa. Koma lomba nimayamikila mwayi umene nakhala nawo wotumikila pa Beteli. Nikhulupilila kuti ngati munthu amavomeleza utumiki uliwonse umene wapatsidwa ngakhale umene saukonda, Yehova nthawi zonse amamudalitsa. Ku Beteli, n’nali kugwila nchito zosiyana-siyana, monga ya mu ofesi, yolonga mabuku, yophika, ndi yoyeletsa. Panthawi ina, anatitumanso kukacita nchito yoyang’anila cigawo, ndipo tinali na mwayi wodziŵana ndi abale na alongo osiyana-siyana m’dziko la Ireland. Kuwonjezela pa izi, tinaona maphunzilo athu a Baibo akupita patsogolo. Zonsezi zinathandiza kuti tizikondana kwambili ndi abale na alongo a m’dzikolo. Linali dalitso lalikulu kwambili!
COCITIKA CAPADELA CA MBONI ZA YEHOVA KU IRELAND
Mu 1965, m’dziko la Ireland munacitika msonkhano woyamba wa maiko. Msonkhanowo unacitikila ku Dublin.b Ngakhale kuti panthawiyo kunali citsutso coopsa, msonkhanowo unayenda bwino. Panapezeka anthu 3,948, ndipo okwana 65 anabatizika. Mwa anthu amenewa, panali abale na alongo okwana 3,500 ocokela ku maiko ena. Aliyense amene analandilako alendowo na kuwapatsa malo ogona, anapatsiwa kalata yomuyamikila. Komanso, olandila alendowo anayamikila kwambili khalidwe labwino la abale ocokela m’maiko ena. Kuyambila nthawiyi, zinthu zinasintha kwambili ku Ireland.
Arthur akupeleka moni kwa M’bale Nathan Knorr atangofika pamsonkhano wacigawo wa mu 1965
Mu 1983, Arthur atulutsa buku lakuti Buku Langa la Nkhani za M’baibo la Cigaeliki
Mu 1966, ofesi ya nthambi ya ku Dublin inayamba kuyang’anila cigawo ca kumpoto ndi ca kum’mwela kwa Ireland. Izi zinacititsa kuti abale na alongo akhale ogwilizana kwambili. Zimenezi zinali zosiyana kwambili ndi anthu ena a m’dzikolo amene anali ogaŵikana cifukwa cosiyana maganizo m’zandale na m’zacipembedzo. Tinali okondwa ngako kuona Akatolika ambili akubwela m’coonadi na kuyamba kutumikila pamodzi na abale amene poyamba anali Apulotesitanti.
UTUMIKI WATHU UNASINTHILATU
Mu 2011, zinthu zinasintha kwambili mu umoyo wathu pamene ofesi ya nthambi ya Britain ndi ya Ireland zinaphatikiziwa pamodzi. Ise tinauziwa kuti tikatumikile ku Beteli ya ku London. Pamene uthengawu unali kutifika, n’nali n’tayamba kale kudela nkhawa za thanzi la Arthur. Iye anamupeza na matenda a manjenje. Pa May 20, 2015, mwamuna wanga amene n’nakhala naye m’cikwati zaka 66, anamwalila.
M’zaka zapitazi, nakhala nikupsinjika maganizo ndi kuvutika na cisoni. Arthur anali kunilimbikitsa nthawi zonse. Nimamuyewa ngako! Koma mavuto onse amene napitamo, anicititsa kuyandikila kwambili kwa Yehova. Nimalimbikitsidwa kudziŵa kuti anthu ambili anali kumukonda Arthur. Nakhala nikulandila makalata ocokela kwa abale na alongo a ku Ireland, Britain, kuphatikizapo a ku America. Makalatawa amanilimbikitsa kwambili. Napindulanso ngako na cilimbikitso cocokela kwa Dennis mng’ono wake wa Arthur, mkazi wake, komanso Ruth na Judy, ana a mlongosi wanga.
Lemba limene limanilimbikitsa ngako ni Yesaya 30:18. Limati: “Yehova azidzayembekezela kuti akukomeleni mtima ndipo adzanyamuka kuti akucitileni cifundo, pakuti Yehova ndi Mulungu amene amaweluza mwacilungamo. Odala ndi anthu onse amene amamuyembekezela.” Kukamba zoona, nimatonthozedwa kudziŵa kuti Yehova akuyembekezela moleza mtima kuti adzathetse mavuto athu na kudzatipatsa nchito yokondweletsa m’dziko latsopano.
Nakhala nikuona mmene Yehova watsogolela ndi kudalitsa nchito yolalikila ku Ireland. Nimaona kuti unali mwayi waukulu kutengako mbali popititsa patsogolo nchito imeneyi. Kukamba zoona, kucita zimene Yehova amafuna, nthawi zonse kumabweletsa madalitso.