LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp18 na. 2 masa. 14-15
  • Tsogolo Lanu Limadalila pa Zosankha Zanu!

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tsogolo Lanu Limadalila pa Zosankha Zanu!
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • SANKHANI KUKONDA MULUNGU
  • MVELANI MAU AKE
  • MUSALEKANE NAYE MULUNGU
  • COSANKHA NI CANU
  • Mungasankhe Mmene Tsogolo Lanu Lidzakhalile
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Khalani Pafupi Ndi Yehova
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Timam’konda Kwambili Atate Wathu Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Izi Ndi Zimene “Kukonda Mulungu Kumatanthauza”
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
wp18 na. 2 masa. 14-15
Mphambano ya msewu

Tsogolo Lanu Limadalila pa Zosankha Zanu!

KODI PALI ZIMENE MUNGACITE NA MMENE MOYO WANU UDZAKHALILA M’TSOGOLO? Anthu ena amakhulupilila kuti umoyo wawo unakonzedwelatu ndipo sangausinthe. Akalephela kukwanilitsa zolinga zawo, amaleka zimene anali kucita pofuna kuzikwanilitsa. Amakamba kuti: “Cinalembeka kale kuti sinizakwanilitsa!”

Ena amakhumudwa akaona kuti sangapewe kupondelezana kumene kuli m’dzikoli lopanda cilungamo. Amayesetsa kuti akhaleko na umoyo wabwino, koma nkhondo, masoka a zacilengedwe, na matenda, zimasokoneza mapulani awo nthawi na nthawi. Amadzifunsa kuti: ‘Kodi nivutikila ciani kufuna kukhala na umoyo wabwino?’

N’zoona kuti zocitika mu umoyo zingasokoneze mapulani athu. (Mlaliki 9:11) Komabe, kuti mukakhale na moyo wamuyaya, zimadalila pa zosankha zanu maka-maka. Ndipo Baibo imafotokozanso zimenezi. Onani zimene imakamba.

Moimilako Yehova, Mose mtsogoleli wa mtundu wa Isiraeli wakale, anauza anthuwo ali pafupi kungena m’Dziko Lolonjezedwa kuti: “Ndaika moyo ndi imfa, dalitso ndi tembelelo pamaso panu. . . . Conco inuyo ndi mbadwa zanu musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo. Musankhe moyo mwa kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvela mawu ake ndi kum’mamatila.”—Deuteronomo 30:15, 19, 20.

“Ndaika moyo ndi imfa, dalitso ndi tembelelo pamaso panu . . . Conco inuyo . . . musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.” —Deuteronomo 30:19

Ndithudi, Mulungu anamasula Aisiraeli mu ukapolo ku Iguputo, na kuŵapatsa ciyembekezo ca umoyo wamtendele ndi wacimwemwe m’Dziko Lolonjezedwa. Koma kuti akakhale na umoyo umenewo pali zimene anafunika kucita. Iwo anafunika ‘kusankha moyo.’ Motani? ‘Mwa kukonda Mulungu, kumvela mau ake ndi kum’mamatila.’

Mofananamo, na imwe mufunika kupanga cosankha masiku ano. Ndipo zimene mudzasankha zidzakhudza tsogolo lanu. Mwa kusankha kukonda Mulungu, kumumvela, na kum’mamatila, ndiye kuti mukusankha kukhala na moyo. Inde, moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Kodi cofunika n’ciani pa lililonse la masitepu amenewa?

SANKHANI KUKONDA MULUNGU

Cikondi ni khalidwe lalikulu la Mulungu. Mouzilidwa, mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:8) Ndiye cifukwa cake Yesu atafunsidwa kuti lamulo lalikulu pa malamulo onse ni liti, iye anayankha kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mateyu 22:37) Conco, ubwenzi wolimba na Yehova Mulungu ufunika kuzikidwa pa cikondi, osati kumumvela cifukwa ca mantha kapena mwacimbuli-mbuli. Nanga n’cifukwa ciani tifunika kusankha kum’konda?

Cikondi ca Yehova pa anthu cili monga cikondi ca makolo pa ana awo. Ngakhale kuti ni opanda ungwilo, makolo acikondi amaphunzitsa, kulimbikitsa, kuthandiza, na kupeleka cilango kwa ana awo, cifukwa amafuna kuti akhale na umoyo wacimwemwe komanso waphindu. Koma kodi makolo amayembekezela ana awo kuwacitila ciani? Iwo amafuna kuti aziwakonda na kusunga pamtima zimene amawaphunzitsa kuti ziwapindulitse. Kodi sizomveka kuti Atate wathu wakumwamba amene ni waungwilo amayembekezela kuti ise tizimukonda na kumuyamikila pa zabwino zonse zimene amaticitila?

MVELANI MAU AKE

M’citundu coyambilila cimene Baibo inalembewa, liu lakuti “kumvela” nthawi zambili limatanthauza ‘kutsatila.’ Kodi sindiye zimene timatanthauza tikauza mwana kuti, “Uzimvela makolo ako”? Conco, kumvela Mulungu kumatanthauza kuphunzila na kutsatila zimene iye amakamba. Popeza sitingamvele Mulungu akamba naise mwacindunji, timamvela iye mwa kuŵelenga na kucita zimene Mau ake Baibo amakamba.—1 Yohane 5:3.

Poonetsa kufunika komvela mau a Mulungu, Yesu pa nthawi ina anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi cakudya cokha, koma ndi mau onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mateyu 4:4) Monga mmene cakudya cilili cofunika m’thupi lathu, kuphunzila za Mulungu n’kofunika kwambili. Cifukwa? Mfumu ya nzelu Solomo inafotokoza kuti: “Nzelu zimateteza monga mmene ndalama zimatetezela, koma ubwino wa kudziwa zinthu ndi wakuti nzelu zimasunga moyo wa eni nzeluzo.” (Mlaliki 7:12) Kukhala na cidziŵitso komanso nzelu zocokela kwa Mulungu, kungatiteteze m’nthawi ino na kutithandiza kupanga cosankha canzelu cimene cingatitsogolele kukapeza moyo wosatha m’tsogolo.

MUSALEKANE NAYE MULUNGU

Kumbukilani fanizo la Yesu limene takambilana m’nkhani yapita. Iye anakamba kuti: “Cipata colowela ku moyo n’copapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owelengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Mosakaikila, kuti tiyende pa njila imeneyi tingapindule kwambili kukhala pafupi na wotitsogolela wodziŵa bwino njila imeneyo kuti tikafike kumene tiyenda, kumene ni ku moyo wosatha. Conco, tili na cifukwa cabwino copitilizila kukhala pa ubwenzi wolimba na Mulungu. (Salimo 16:8) Nanga tingacite ciani kuti tikhalebe naye pa ubwenzi?

Tsiku na tsiku pali zinthu zambili zimene timafunika kucita komanso zina zambili zimene ise tingakonde kucita. Zinthu monga zimenezo zingatipangitse kukhala bize cakuti tingakhale na nthawi yocepa kapena kukhala tilimbiletu nthawi yoganizila zimene Mulungu amafuna kuti ticite. Ndiye cifukwa cake, Baibo imatikumbutsa kuti: “Samalani kwambili kuti mmene mukuyendela si monga anthu opanda nzelu, koma ngati anzelu. Muzigwilitsa nchito bwino nthawi yanu cifukwa masikuwa ndi oipa.” (Aefeso 5:15, 16) Timapitiliza kukhala pa ubwenzi na Mulungu mwa kuona ubwenzi wathu na iye kukhala cinthu cofunika kwambili mu umoyo wathu.—Mateyu 6:33.

COSANKHA NI CANU

Olo kuti simungasinthe zinthu zimene zinacitika kale, pali zimene mungacite kuti imwe na okondedwa anu mukhale na tsogolo labwino. Baibo imafotokoza kuti Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu amatikonda kwambili ndipo amatiuza zimene iye amafuna kuti ise tizicita. Onani mau awa a mneneli Mika:

“Iye anakuuza zimene zili zabwino. Kodi Yehova akufuna ciyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzicita cilungamo, ukhale wokoma mtima ndiponso uziyenda modzicepetsa ndi Mulungu wako.”—Mika 6:8.

Kodi mudzavomela ciitano ca Yehova cakuti muyende naye na kuti mukapeze madalitso osatha amene wasungila anthu amene avomela ciitano? Cosankha ni canu!

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani