Maulaliki Acitsanzo
NSANJA YA MLONDA March-April
Tikugaŵila kapepala ka uthenga aka kwa aliyense. [Patsani mwininyumba kapepala kakuti Kodi Baibo Mumaiona Bwanji? ndi kum’funsa mafunso ali patsambo loyamba. Musonyezeni yankho la m’Baibulo pa 2 Timoteyo 3:16 ndi kumulimbikitsa kuti apeze nthawi yoŵelenga kapepalako.] Ena amakaikila ngati Baibulo lili ndi malangizo amene angawathandize pankhani ya nchito yao? Onani zimene Baibulo limanena pankhani ya nchito. [Ŵelengani Mlaliki 3:13.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuti tizisangalala ndi nchito. Kodi ndingakusiileni magaziniyi?
Galamukani! April
Lelo tikuceza ndi mabanja mwacidule. Anthu ambili amada nkhawa ndi kusintha kumene amaona m’mabanja. Kale ana anali kumvela makolo koma tsopano m’mabanja ena, ana samvela makolo. Kodi muganiza kuti makolo asiya kulangiza ana ao? [Yembekezani yankho.] Malinga ndi zimene Baibulo limanena cilango n’cofunika kwambili. [Ŵelengani Miyambo 29:17.] Magazini ino ifotokoza malangizo othandiza pa kupeleka cilango kwa ana.”