LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb17 March tsa. 5
  • Kuseŵenzetsa Kabuku ka Mvetselani kwa Mulungu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kuseŵenzetsa Kabuku ka Mvetselani kwa Mulungu?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Tingagwilitsile Nchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu!
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Seŵenzetsani Buku Lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! mu Ulaliki
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kuti Akakhale Ophunzila Obatizika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Mmene Tingagwilitsile Nchito Kabuku kakuti Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano?
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
mwb17 March tsa. 5

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kuseŵenzetsa Kabuku ka Mvetselani kwa Mulungu?

Mvetselani kwa Mulungu

Kabuku ka Mvetselani kwa Mulungu anakakonza kuti tiziphunzitsila anthu mfundo zoyambilila za m’Baibo. Mapikica ake amathandiza kwambili anthu amene sakwanitsa kuŵelenga bwino-bwino. Phunzilo iliyonse ya pamapeji aŵili ili na mapikica okhala na tumivi tolongoza makambilano kucoka pa pikica ina kupita pa yotsatila.

Kabuku ka Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Kwamuyaya kali na mapikica amene alinso mu Mvetselani kwa Mulungu, koma kali na mau oculukilapo. Ophunzila amene amakwanitsako kuŵelenga bwino angaseŵenzetse kameneka. Nthawi zambili ofalitsa amakonda kukaseŵenzetsa monga buku la mphunzitsi, pamene wophunzila wawo aseŵenzetsa ka Mvetselani kwa Mulungu. Mapeji ambili ali na kabokosi ka mfundo zowonjezela, ndipo mungakambilane mfundozo malinga ndi wophunzila wanu.

Mlongo aseŵenzetsa kabuku ka Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Kwamuyaya pamene wophunzila wake aseŵenzetsa ka Mvetselani kwa Mulungu

Mungagaŵile tumabuku tumenetu panthawi iliyonse, ngakhale kuti si cogaŵila ca mwezi umenewo. Potsogoza phunzilo la Baibo, seŵenzetsani mapikica kuti mufotokoze nkhani za m’Baibo. Funsani mafunso kuti muloŵetsemo wophunzila ndi kutsimikizila kuti wamvetsetsa. Ŵelengani ndi kukambilana malemba ali pansi pa peji iliyonse. Mukakatsiliza kuphunzila kabukuka, kayambeni naye buku lakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse kuti mukam’thandize kupita patsogolo ndi kukabatizika.

Zimene tiphunzila pa nkhani ya Adamu na Hava m’munda wa Edeni m’kabuku ka Mvetselani kwa Mulungu
    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani