Nyimbo 110
Ntchito Zodabwitsa za Mulungu
(Salimo 139)
1. Inu Mulungu mumadziwa
Ndikagona ndipo ndikadzuka.
Mumadziwanso maganizo anga
Ngakhale mawu anga
Ndi njira zanga.
Munaona malo ’bisika.
Panthawi yomwe ndinali m’mimba.
Ziwalo zangatu zinalembedwa,
Ndikutamandani ndinu wodabwitsa.
Nzeru zanu Mulungu n’zodabwitsa.
Zimenezi ndithu ndikudziwa.
Ndikaopa kuphimbidwa ndi mdima
Mzimu wanu M’lungu undipeza.
N’kuti komwe ndingabisale
Komwe inu simungandione?
Kumwamba kodi kapena kumanda,
Mumdima, m’nyanja?
Ayi ndithu kulibe.
(Onaninso Sal. 66:3; 94:19; Yer. 17:10.)