NYIMBO 21
Pitilizani Kufuna-funa Ufumu Coyamba
Yopulinta
1. Yehova asangalala,
Na Ufumu wa Khristu.
Adzaugwilitsa nchito,
Kukonza zinthu zonse.
(KOLASI)
M’fune Ufumu coyamba,
Na cilungamo cake.
Tumikilani Yehova
Ndipo mutamandeni.
2. M’fune Ufumu coyamba,
M’malo modela nkhawa.
Kuti maŵa tidya ciani,
Dalilani Yehova.
(KOLASI)
M’fune Ufumu coyamba,
Na cilungamo cake.
Tumikilani Yehova
Ndipo mutamandeni.
3. Lalikilani uthenga;
Onse adziŵe kuti,
Adzapeza madalitso
Mu Ufumu wa M’lungu.
(KOLASI)
M’fune Ufumu coyamba,
Na cilungamo cake.
Tumikilani Yehova
Ndipo mutamandeni.
(Onaninso Sal. 27:14; Mat. 6:34; 10:11, 13; 1 Pet. 1:21.)