Kodi Mudzacita Ciani Panthawi ya Maholide?
Popeza kuti anthu ambili amakhala panyumba panthawi ya maholide acipembedzo ndi maholide ena, imeneyi imakhala nthawi yabwino yolalikila. Mipingo ikulimbikitsidwa kupanga makonzedwe apadela kuti ikalalikile panthawi ya maholide. Popeza kuti anthu ambili m’gawo aziuka mocedwa, ndi bwino kusintha nthawi yokonzekela kupita mu ulaliki. Ngati n’kotheka, pa Msonkhano wa Nchito mungapeleke cilengezo codziŵitsa mpingo za makonzedwe apadela ocita umboni panthawi ya maholide. Limbikitsani onse amene angathe kuti atengeko mbali pa nchito yocitila umboni. N’zoona kuti maholide amatipatsa mpata wopuma ndi kucita zinthu zaumwini. Koma m’malo mongothela tsiku lonse kucita zinthu zosangulutsa, bwanji osapatula nthawi yocitako ulaliki? Mukacita zimenezi, mudzakhala ndi cimwemwe cimene cimabwela kaamba kocita utumiki wopatulika.—Mat. 11:29, 30.