LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb17 February tsa. 8
  • Thandizani Ana Anu Kukhala na Cikhulupililo Colimba mwa Mlengi Wawo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Thandizani Ana Anu Kukhala na Cikhulupililo Colimba mwa Mlengi Wawo
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Nkhani Zofanana
  • Pendani Umboni
    Galamuka!—2021
  • 12 Zolinga
    Galamuka!—2018
  • Thandizo Ilipo
    Galamuka!—2020
  • Anagonjetsa Tsankho
    Galamuka!—2020
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
mwb17 February tsa. 8

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Thandizani Ana Anu Kukhala na Cikhulupililo Colimba mwa Mlengi Wawo

Cilengedwe cimalengeza ulemelelo wa Yehova. (Sal. 19:1-4; 139:14) Koma dziko la Mdyelekezi limalimbikitsa ziphunzitso zotsutsa mfundo yakuti Mulungu ndiye anapanga moyo. (Aroma 1:18-25) Kodi mungateteze bwanji ana anu ku ziphunzitso zimenezo kuti zisazike mizu m’maganizo na m’mitima yawo? Ayambilileni ali aang’ono. Athandizeni kukhulupilila kuti Yehova aliko, ndipo amasamala za iwo aliyense payekha-payekha. (2 Akor. 10:4, 5; Aef. 6:16) Yesani kudziŵa zimene iwo amaganiza pa zinthu zimene amaphunzila ku Sukulu. Ndiyeno seŵenzetsani zida zambili zimene tili nazo kuti muwafike pamtima.—Miy. 20:5; Yak. 1:19.

Tate aphunzitsa ana ake za cilengedwe; aphunzila za cisanduliko m’kilasi; Zimene Acicepele Anzanu Amakamba—Kukhulupilila mwa Mulungu

TAMBANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE ACICEPELE ANZANU AMAKAMBA—KUKHULUPILILA MWA MULUNGU, NDIYENO KAMBILANANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi ambili amati ciani pa nkhani yokhulupilila Mulungu?

  • Nanga kusukulu kwanu amaphunzitsa ciani pa nkhani imeneyi?

  • N’ciani cimakukhutilitsani kuti Yehova aliko?

  • Mungam’thandize bwanji munthu wina kukhulupilila kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse?

ZIDA ZINA ZIMENE ZILIPO:

• Nkhani za pa JW.ORG “Zimene Ndimaphunzila m’Baibo” (A zaka zitatu kubwela pansi)

• Vidiyo Khala Bwenzi la Yehova—“Yehova  . . Analenga Zinthu Zonse”

• Nkhani za mu Galamukani! “Kodi Zinangocitika Zokha?”

• Mapepa Olembapo a pa JW.ORG “N’chifukwa Chiyani Ndimakhulupirira Zoti Kuli Mulungu?”

• Nkhani za pa JW.ORG “Kodi Zinthu zinacita kulengedwa?” (Zigawo 4)

• Mavidiyo a pa JW Broadcasting “Maganizo a Anthu pa Nkhani Yokhudza Mmene Moyo Unayambila”

• Vidiyo The Wonders of Creation Reveal God’s Glory

• Kabuku Was Life Created?

• Buku Is There a Creator Who Cares About You??

The Origin of Life—Five Questions Worth Asking

The Origin of Life—Five Questions Worth Asking

Colinga ca kabukuka n’kuthandiza maka-maka Mboni zacicepele zimene zimaphunzitsidwa za cisanduliko kusukulu kwawo. Tingakagaŵilenso kwa anthu amene angafune kudziŵa za umboni weni-weni wakuti kuli Mlengi.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani