UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Mumadziimbabe Mlandu?
Kungakhale kovuta kuleka kudziimba mlandu pa zolakwa zimene Yehova anatikhululukila kale. Nkhani imeneyi inakambiwa pa msonkhano wa cigawo wa mu 2016 wa mutu wakuti “Khalanibe Wokhulupilika kwa Yehova.” Ndipo tinatamba vidiyo yokhudza zimenezi. Seŵenzetsani JW Library kuti mutambenso vidiyo imeneyo na kuyankha mafunso aya:
Kodi Soniya anakhala wocotsedwa kwa utali wanji?
Ni lemba liti limene akulu anamuŵelengela? Nanga inam’thandiza bwanji?
Soniya atabwezedwa, kodi mpingo unamulandila bwanji?
Ni maganizo ati amene Soniya analimbana nawo, nanga atate ake anam’thandiza bwanji?