CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Mmene Cilamulo Cinaonetsela Kuti Yehova Amawadela Nkhawa Akazi
Mwamuna akakwatila sanayenele kupita kunkhondo n’kusiya mkazi wake m’caka coyamba ca ukwati wawo (Deut. 24:5; it-2 1196 ¶4)
Akazi amasiye anali kusamalidwa mwakuthupi (Deut. 24:19-21; it-1 963 ¶2)
Akazi amasiye amene analibe ana anali kupatsidwa mwayi wokwatiwa kuti abeleke ana (Deut. 25:5, 6; w11 3/1 23)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi m’banja langa kapena mu mpingo, ningaonetse bwanji kuti akazi nimaaganizila?’