NYIMBO 76
Kodi Mumamvela Bwanji?
(Aheberi 13:15)
1. Mumamvela bwanji,
polalikila ena,
Na kuphunzitsa anthu
okonda co’nadi?
Ngati simuleka,
M’lungu adzadalitsa.
Mudzathandiza anthu
kudziŵa Yehova.
(KOLASI)
Ise timasangalala
kudzipeleka kwa M’lungu.
Ndiponso sitidzaleka
Kum’tamanda iye.
2. Mumamvela bwanji
kuona kuti anthu
Akumvetsela uthenga
wopatsa moyo?
Ena amakana,
safuna na kumvela.
Koma ise sitileka
kulalikila.
(KOLASI)
Ise timasangalala
kudzipeleka kwa M’lungu.
Ndiponso sitidzaleka
Kum’tamanda iye.
3. Mumamvela bwanji
kuona kuti M’lungu,
Adzakuthandizani
kuti mupambane?
Timalalikila
na kuphunzitsa anthu,
Tifuna kuti
nawo akapulumuke.
(KOLASI)
Ise timasangalala
kudzipeleka kwa M’lungu.
Ndiponso sitidzaleka
Kum’tamanda iye.
(Onaninso Mac. 13:48; 1 Ates. 2:4; 1 Tim. 1:11.)