LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 January tsa. 11
  • Sankhani Kutumikila Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Sankhani Kutumikila Yehova
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Ubatizo ni Khomo la ku Madalitso Oculuka!
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Ubatizo Ni Wofunika kwa Mkhristu Aliyense
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Kodi Ubatizo Ndi Wofunika Bwanji Paubwenzi Wanu ndi Mulungu?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kodi Ndimwe Wokonzeka Kubatizika?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 January tsa. 11
Msewu wokhota-khota woimilako njila yotumikila Yehova. Zikwangwani zimene zili mbali mwa njilayo ziimila masitepe amene ni kuphunzila Baibo, kupezeka pamisonkhano, kulalikila, na kubatizika.

Kodi imwe mwafika pati pa njila yopita kukabatizika?

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Sankhani Kutumikila Yehova

Ngati ndimwe Mkhristu wacinyamata wosabatizika kapena wophunzila Baibo, kodi muli na colinga cokabatizika? N’cifukwa ciani muyenela kubatizika? Kudzipatulila na kubatizika kudzakuthandizani kukhala pa ubale wapadela na Yehova. (Sal. 91:1) Kudzakuthandizaninso kuti mukapulumuke. (1 Pet. 3:21) N’ciani cingakuthandizeni kuti mufike pa kudzipatulila na kubatizika?

Muyenela kukhutila inu mwini kuti zimene muphunzila ni coonadi. Mukakhala na mafunso, fufuzani. (Aroma 12:2) Dziŵani mbali zimene mungafunike kuwongolela, ndipo sinthani n’colinga cakuti mukondweletse Yehova. (Miy. 27:11; Aef. 4:23, 24) Nthawi zonse muzipemphela kwa iye kuti akuthandizeni. Khalani otsimikiza kuti Yehova adzakulimbitsani na kukucilikizani na mphamvu yake ya mzimu woyela. (1 Pet. 5:10, 11) Mukayesetsa mwakhama mudzapindula. Kutumikila Yehova ndiko kofunika kwambili pa umoyo!—Sal. 16:11.

ONETSANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE MUNGACITE KUTI MUYENELELE UBATIZO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi ena agonjetsa zopinga zanji kuti ayenelele ubatizo?

  • Mungacite ciani kuti mukhale na cikhulupililo cofunikila kuti mudzipatulile kwa Yehova?

  • N’ciani casonkhezela ena kupanga masinthidwe ofunikila kuti ayenelele ubatizo?

  • Kodi Yehova amawadalitsa bwanji anthu amene amasankha kum’tumikila?

  • Kodi kudzipatulila na kubatizika kutanthauza ciani?

Kumapeto kwa nkhani ya ubatizo, mkambi amapempha opita ku ubatizo kuti aimilile na kuyankha mafunso aŵili otsatilawa mokweza:

Kodi munalapa macimo anu, kudzipatulila kwa Yehova na kuvomeleza njila yake yacipulumutso kupitila kwa Yesu Khristu?

Kodi mukumvetsa kuti mukabatizika lelo, ndiye kuti mwadziŵika kukhala Mboni ya Yehova, yogwilizana na gulu lake?

Opita ku ubatizo akayankha movomeleza mafunso amenewa, amalengeza poyela kuti amakhulupilila nsembe ya dipo, komanso kuti anadzipatulila kothelatu kwa Yehova.—Aroma 10:9, 10.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani