Cisanu, October 17
Pitilizani kuyenda ngati ana a kuwala.—Aef. 5:8.
Timafunikila thandizo la mzimu wa Mulungu kuti tipitilize kucita zinthu “ngati ana a kuwala.” Cifukwa ciyani? Cifukwa si copepuka kukhalabe woyela m’dziko lino lodzala na makhalidwe oipa. (1 Ates. 4:3-5, 7, 8) Mzimu woyela ungatithandize kugonjetsa maganizo a m’dzikoli amene amasemphana na kaganizidwe ka Mulungu. Mzimuwo ungatithandizenso kubala cipatso “ciliconse cabwino ndi ciliconse colungama.” (Aef. 5:9) Njila imodzi imene tingalandile mzimu woyela ni kuupempha. Yesu ananena kuti Yehova “adzapeleka mowolowa manja mzimu woyela kwa amene akumupempha.” (Luka 11:13) Timalandilanso mzimu woyela tikamatamanda Yehova capamodzi pa misonkhano yathu. (Aef. 5:19, 20) Cisonkhezelo cabwino cimene mzimu woyela umakhala naco pa ife cimatithandiza kukhala na umoyo wokondweletsa Mulungu. w24.03 23-24 ¶13-15
Ciŵelu, October 18
Pitilizani kupempha ndipo adzakupatsani. Pitilizani kufunafuna ndipo mudzapeza. Pitilizani kugogoda ndipo adzakutsegulilani.—Luka 11:9.
Kodi mufunika kukulitsa kuleza mtima? Ngati n’telo, ipempheleleni nkhaniyo. Kuleza mtima ni cipatso cimene mzimu woyela umabala. (Agal. 5:22, 23) Conco, tiyenela kupempha mzimu woyela wa Yehova kuti utithandize kukulitsa cipatso cimeneci. Kuleza mtima kwathu kukakhala pa mayeso, ‘tidzapemphabe’ mzimu woyela kuti utithandize kukhala oleza mtima. (Luka 11:13) Tingapemphenso Yehova kuti atithandize kuona zinthu mmene iye amazionela. Pambuyo popemphela, tiyenela kuyesetsa kukhala oleza mtima tsiku lililonse. Tikamapemphela kwambili kuti tikhale oleza mtima, na kuyesetsa kukhala otelo, khalidweli lidzazika mizu mumtima mwathu. Ndipo lidzakhala umunthu wathu. Zingakhalenso zothandiza kusinkhasinkha zitsanzo za m’Baibo. M’Baibo muli zitsanzo zambili za anthu amene anali oleza mtima. Tikamasinkhasinkha zitsanzo zimenezo, tidzaphunzila mmene tingaonetsele kuleza mtima. w23.08 22 ¶10-11
Sondo, October 19
Muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.—Luka 5:4.
Yesu anam’tsimikizila mtumwi Petulo kuti Yehova adzam’thandiza. Iye ataukitsidwa, anacitanso cozizwitsa kwa Petulo na atumwi anzake powathandiza kupha nsomba. (Yoh. 21:4-6) Mosakayikila, cozizwitsa cimeneci cinatsimikizila Petulo kuti Yehova adzasamalila zosoŵa zake zakuthupi. N’kutheka kuti mtumwiyu anakumbukila mawu a Yesu akuti Yehova adzasamalila anthu amene ‘apitiliza kufuna-funa Ufumu coyamba.’ (Mat. 6:33) Izi zinapangitsa Petulo kuika utumikila patsogolo m’malo mwa nchito yake ya usodzi. Iye molimba mtima analalikila pa Pentekosite mu 33 C.E., ndipo anthu masauzande analabadila uthenga wabwino. (Mac. 2:14, 37-41) Pambuyo pake, iye anathandiza Asamariya na anthu amitundu ina kuphunzila za Khristu na kum’tsatila. (Mac. 8:14-17; 10:44-48) Zoonadi, Yehova anam’gwilitsa nchito kwambili pokoka anthu a mitundu yonse kuti abwele mu mpingo. w23.09 20 ¶1; 23 ¶11