-
Yeremiya 25:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Choncho ndinatenga kapu imene inali mʼdzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse imene Yehova ananditumizako. Mitunduyo ndi iyi:+
-
-
Yeremiya 25:22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 mafumu onse a Turo, mafumu onse a Sidoni+ ndi mafumu a pachilumba chamʼnyanja.
-
-
Ezekieli 26:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndikuukira iwe Turo ndipo ndikutumizira mayiko ambiri kuti adzamenyane nawe. Iwo adzabwera ngati mafunde amʼnyanja.
-
-
Ezekieli 27:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira yokhudza Turo.+
-
-
Amosi 1:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Yehova wanena kuti,
‘Popeza Turo anandigalukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa.
Chifukwa anapereka ku Edomu gulu lonse la anthu ogwidwa ukapolo,
Ndiponso chifukwa chakuti sanakumbukire pangano la pachibale.+
10 Choncho ndidzatumiza moto pampanda wa Turo,
Ndipo udzawotcheratu nsanja zake zolimba.’+
-
-
Zekariya 9:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Turo anamanga malo okwera omenyerapo nkhondo.
Anadziunjikira siliva wambiri ngati fumbi,
Ndiponso golide wambiri ngati dothi lamʼmisewu.+
-