Yobu
8 Kenako Bilidadi wa ku Shuwa+ anati:
2 “Kodi ukhala ukulankhula zimenezi mpaka liti,+
Pamene zolankhula za m’kamwa mwako zili ngati mphepo yamphamvu?+
4 Ngati ana ako amuchimwira,
Mwakuti iye wawalanga chifukwa cha kupanduka kwawo,
Ndi kuchonderera Wamphamvuyonse,
6 Ngati uli woyera ndi wowongoka mtima,+
Bwenzi panopa atadzuka kuti akumvere,
Ndipo ndithu akanabwezeretsa malo ako olungama pamene unali kukhala.
7 Komanso chiyambi chako chikanaoneka ngati chaching’ono,
Koma mapeto ako akanakhala aakulu kwambiri.+
9 Pakuti ife tabadwa dzulo,+ ndipo sitikudziwa kalikonse,
Chifukwa masiku athu padziko lapansi ali ngati mthunzi.+
10 Kodi iwo sadzakulangiza, sadzakuuza?
Ndipo kodi iwo sadzalankhula kuchokera mumtima mwawo?
11 Kodi gumbwa*+ amamera n’kutalika pamalo pamene si padambo?
Ndipo kodi bango limakula popanda madzi?
13 Ndi mmene zilili njira za onse oiwala Mulungu,+
Ndipo chiyembekezo cha wampatuko chidzatha.+
14 Iye amene chidaliro chake chimatha,
15 Iye adzatsamira nyumba yake, koma siidzakhala chiimire.
Adzaigwira, koma siidzakhalitsa.
16 Iye ali ngati chomera chachiwisi bwino chomwe chikuwombedwa dzuwa.
M’munda mwake, nthambi zake zimakula.+
17 Mizu yake imapiringizanapiringizana pamulu wa miyala.
Iye amaona kuti miyalayo ndi nyumba yake.