Genesis 35:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Pomalizira pake, pamene moyo wake+ unali kutayika (pakuti anamwalira),+ anatcha mwanayo dzina lakuti Beni-oni.* Koma bambo ake anamutcha Benjamini.*+ Genesis 42:38 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 38 Komabe bambo awo anati: “Zoti mwana wanga apite nanu, izo ndakana, chifukwa m’bale wake anafa, ndipo iye anatsala yekha.+ Ngati angakumane ndi tsoka n’kufa panjira, ndithu mudzatsitsira ku Manda+ imvi zanga ndi chisoni.” Genesis 44:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Ife tinakuyankhani mbuyanga kuti, ‘Bambo tili nawo koma ndi okalamba. Ali ndi mwana amene anabereka atakalamba, amene ndiye wamng’ono pa ife tonse.+ M’bale wake wa mimba imodzi anamwalira, moti anatsala yekha,+ ndipo bambo amam’konda kwambiri.’
18 Pomalizira pake, pamene moyo wake+ unali kutayika (pakuti anamwalira),+ anatcha mwanayo dzina lakuti Beni-oni.* Koma bambo ake anamutcha Benjamini.*+
38 Komabe bambo awo anati: “Zoti mwana wanga apite nanu, izo ndakana, chifukwa m’bale wake anafa, ndipo iye anatsala yekha.+ Ngati angakumane ndi tsoka n’kufa panjira, ndithu mudzatsitsira ku Manda+ imvi zanga ndi chisoni.”
20 Ife tinakuyankhani mbuyanga kuti, ‘Bambo tili nawo koma ndi okalamba. Ali ndi mwana amene anabereka atakalamba, amene ndiye wamng’ono pa ife tonse.+ M’bale wake wa mimba imodzi anamwalira, moti anatsala yekha,+ ndipo bambo amam’konda kwambiri.’