18 Kenako, chakacho chinafika kumapeto, ndipo anthu anayamba kufika kwa iye chaka chotsatira. Iwo ankanena kuti: “Sitikubisirani mbuyathu, ndalama zathu ndi ziweto zonse zathera kwa inu.+ Zimene tangotsala nazo ndi matupi athuwa ndi nthaka yathuyi basi.+