Genesis 12:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Ine ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe. Ndidzakudalitsa ndi kukuza dzina lako, ndipo iwe ukhale dalitso+ kwa ena. Genesis 15:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Kenako anamutengera panja, n’kumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.”+ Ndipo anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.”+ Ekisodo 1:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Ana a Isiraeli anaberekana ndipo anachuluka m’dzikomo. Iwo anapitiriza kuchulukana ndi kukhala amphamvu koposa, moti anadzaza m’dzikomo.+ Deuteronomo 26:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Pamenepo uzikanena pamaso pa Yehova Mulungu wako kuti, ‘Bambo anga anali Msiriya+ wotsala pang’ono kufa. Anapita ku Iguputo+ ndi anthu ochepa chabe+ a m’banja lake kukakhala kumeneko monga mlendo, koma anakhaladi mtundu waukulu ndi wamphamvu kumeneko.+ Aheberi 11:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Choteronso, kuchokera mwa mwamuna mmodzi,+ amene anali ngati wakufa,+ kunabadwa ana ochuluka ngati nyenyezi zakumwamba komanso osawerengeka ngati mchenga wa m’mbali mwa nyanja.+
2 Ine ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe. Ndidzakudalitsa ndi kukuza dzina lako, ndipo iwe ukhale dalitso+ kwa ena.
5 Kenako anamutengera panja, n’kumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.”+ Ndipo anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.”+
7 Ana a Isiraeli anaberekana ndipo anachuluka m’dzikomo. Iwo anapitiriza kuchulukana ndi kukhala amphamvu koposa, moti anadzaza m’dzikomo.+
5 Pamenepo uzikanena pamaso pa Yehova Mulungu wako kuti, ‘Bambo anga anali Msiriya+ wotsala pang’ono kufa. Anapita ku Iguputo+ ndi anthu ochepa chabe+ a m’banja lake kukakhala kumeneko monga mlendo, koma anakhaladi mtundu waukulu ndi wamphamvu kumeneko.+
12 Choteronso, kuchokera mwa mwamuna mmodzi,+ amene anali ngati wakufa,+ kunabadwa ana ochuluka ngati nyenyezi zakumwamba komanso osawerengeka ngati mchenga wa m’mbali mwa nyanja.+