5 Kenako muzikanena pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Bambo anga anali munthu wongoyendayenda wa Chiaramu+ ndipo anapita ku Iguputo+ ndi anthu ochepa amʼbanja lawo+ nʼkukakhala kumeneko monga mlendo. Koma ali kumeneko anakhala mtundu waukulu ndi wamphamvu.+