Habakuku 2:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Uchite zimenezi pakuti masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu+ ndipo akuthamangira kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengereza, uziwayembekezerabe* chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu.+ Iwo sadzachedwa. 2 Petulo 3:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Yehova sakuchedwa kukwaniritsa lonjezo lake,+ ngati mmene anthu ena amaonera kuti akuchedwa, koma akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.+ Chivumbulutso 7:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Anafuula kuti: “Musawononge dziko lapansi, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira titadinda chidindo+ pamphumi+ za akapolo a Mulungu wathu.”
3 Uchite zimenezi pakuti masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu+ ndipo akuthamangira kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengereza, uziwayembekezerabe* chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu.+ Iwo sadzachedwa.
9 Yehova sakuchedwa kukwaniritsa lonjezo lake,+ ngati mmene anthu ena amaonera kuti akuchedwa, koma akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.+
3 Anafuula kuti: “Musawononge dziko lapansi, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira titadinda chidindo+ pamphumi+ za akapolo a Mulungu wathu.”