Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 26:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Nsalu yotchingayi uipachike m’munsi mwa ngowe zolumikizira nsalu zapamwamba pa chihema, ndipo uike likasa la umboni+ kuseri kwa nsalu yotchingayi. Nsaluyi ikhale malire pakati pa Malo Oyera+ ndi Malo Oyera Koposa.+

  • Ekisodo 40:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Mkati mwake, udzaikemo likasa la umboni+ ndi kutchinga kumene kuli Likasalo ndi nsalu.+

  • Aheberi 6:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Chiyembekezo+ chimene tili nachochi chili ngati nangula* wa miyoyo yathu ndipo n’chotsimikizika ndiponso chokhazikika. Chiyembekezo chimenechi chimatilowetsa mkati, kuseri kwa nsalu yotchinga,+

  • Aheberi 9:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Pakuti panamangidwa chipinda choyamba cha chihema.+ M’chipindamo munali choikapo nyale,+ tebulo,+ ndi mitanda ya mkate woonetsedwa,+ ndipo chinali kutchedwa “Malo Oyera.”+

  • Aheberi 9:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Koma kuseri kwa nsalu yotchinga yachiwiri+ kunali chipinda chinanso chotchedwa “Malo Oyera Koposa.”+

  • Aheberi 10:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Iye ndi amene anatikhazikitsira njira imeneyi monga njira yatsopano ndi yamoyo, yodutsa nsalu yotchinga,+ imene ndi thupi lake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena