8 Ndipo lamba womangira efodi,+ wolumikiza ku efodiyo akhale wopangidwa ndi nsalu ya efodi yomweyo. Akhale wopangidwa ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota, wabwino kwambiri.
20 Ndiyeno anapanga mphete ziwiri zagolide ndi kuziika pansalu ziwiri za pamapewa za efodi m’munsi mwake, kutsogolo kwa nsaluzo, pafupi ndi polumikizira, pamwamba pa lamba wa efodi.+
7 Atatero anaveka Aroni mkanjo+ ndi kum’manga lamba wa pamimba.+ Anamuvekanso malaya odula manja+ komanso efodi,*+ ndi kum’manga kwambiri ndi lamba+ wa efodiyo.