10 Ndiyeno wansembe azivala zovala zake zogwirira ntchito,+ ndi kuvala kabudula wansalu+ wobisa thupi lake. Kenako azichotsa phulusa losakanizika ndi mafuta,+ la nsembe yopsereza imene izitenthedwa pamoto wa paguwa nthawi zonse, ndipo aziika phulusalo pambali pa guwa lansembe.