21 M’chihema chokumanako, kunja kwa nsalu yotchinga+ pafupi ndi Umboni, Aroni ndi ana ake azikhazika nyale pamalo ake, kuunikira pamaso pa Yehova,+ kuyambira madzulo mpaka m’mawa. Limeneli ndi lamulo kwa ana a Isiraeli+ kuti mibadwo yawo izichita zimenezi mpaka kalekale.+