Ekisodo 34:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Kenako iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima, inu Yehova, chonde, Yehova ayende nafe pakati pathu,+ chifukwa anthuwa ndi ouma khosi,+ ndipo mutikhululukire zolakwa zathu ndi machimo athu,+ ndi kutitenga kukhala chuma chanu.”+ Deuteronomo 9:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Muyenera kudziwa kuti Yehova Mulungu wanu akukupatsani dziko labwinoli osati chifukwa cha kulungama kwanu, pakuti ndinu anthu ouma khosi.+ Nehemiya 9:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “Koma iwo, makolo athu, anachita zinthu modzikuza+ moti anaumitsa khosi lawo+ ndipo sanamvere malamulo anu. Machitidwe 7:51 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 51 “Anthu okanika inu ndi osachita mdulidwe wa mumtima+ ndi m’makutu. Nthawi zonse mumatsutsana ndi mzimu woyera. Mmene anachitira makolo anu inunso mukuchita chimodzimodzi.+ Aheberi 3:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Tichite zimenezi pamene Malemba akunena kuti: “Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+ musaumitse mitima yanu ngati mmene zinakhalira pamene makolo anu anandipsetsa mtima.”+
9 Kenako iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima, inu Yehova, chonde, Yehova ayende nafe pakati pathu,+ chifukwa anthuwa ndi ouma khosi,+ ndipo mutikhululukire zolakwa zathu ndi machimo athu,+ ndi kutitenga kukhala chuma chanu.”+
6 Muyenera kudziwa kuti Yehova Mulungu wanu akukupatsani dziko labwinoli osati chifukwa cha kulungama kwanu, pakuti ndinu anthu ouma khosi.+
16 “Koma iwo, makolo athu, anachita zinthu modzikuza+ moti anaumitsa khosi lawo+ ndipo sanamvere malamulo anu.
51 “Anthu okanika inu ndi osachita mdulidwe wa mumtima+ ndi m’makutu. Nthawi zonse mumatsutsana ndi mzimu woyera. Mmene anachitira makolo anu inunso mukuchita chimodzimodzi.+
15 Tichite zimenezi pamene Malemba akunena kuti: “Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+ musaumitse mitima yanu ngati mmene zinakhalira pamene makolo anu anandipsetsa mtima.”+