9 Chihema chimenecho chinali chifaniziro+ cha nthawi yoikidwiratu imene tsopano yafika,+ ndipo mogwirizana ndi chifanizirocho, zonse ziwiri, mphatso ndi nsembe zimaperekedwa.+ Komabe, zimenezi sizipangitsa munthu amene akuchita utumiki wopatulikayo kukhala wangwiro+ m’chikumbumtima chake.+