10 “Mundipangire Likasa la mtengo wa mthethe,+ mikono* iwiri ndi hafu m’litali, mkono umodzi ndi hafu m’lifupi, ndi mkono umodzi ndi hafu msinkhu wake.
27“Upange guwa lansembe la matabwa a mthethe, m’litali mikono isanu, ndipo m’lifupi mikono isanu. Guwalo+ likhale lofanana muyezo wake mbali zake zonse zinayi, ndipo msinkhu wake likhale mikono itatu.