13 Owerengedwa onse ayenera kupereka zotsatirazi: hafu ya sekeli yolingana ndi sekeli la kumalo oyera.*+ Magera* 20 amakwana sekeli limodzi. Hafu ya sekeli ndi chopereka kwa Yehova.+
16 Mwanayo uzimuwombola ndi dipo akakwanitsa mwezi umodzi kapena kuposerapo. Uzimuwombola ndi mtengo woikidwiratu, masekeli asiliva asanu, malinga ndi sekeli la kumalo oyera,+ lofanana ndi magera+ 20.