2 Muzikumbukira njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m’chipululu zaka 40 zonsezi.+ Iye anakuyendetsani m’chipululu kuti akuphunzitseni kudzichepetsa,+ kukuyesani+ pofuna kudziwa zimene zinali mumtima mwanu,+ kuti aone ngati mukanasunga malamulo ake kapena ayi.