37 “Koma mukupitirizabe kukhala ndi moyo chifukwa anakonda makolo anu ndipo anasankha mbewu zawo zobwera pambuyo pawo,+ ndi kukutulutsani mu Iguputo ndi mphamvu zake zazikulu,+ komanso anali kukuyang’anirani.
28 Zoonadi, pa nkhani ya uthenga wabwino iwo ndi adani a Mulungu, ndipo zimenezi zapindulitsa inu.+ Koma kunena za kusankha kwa Mulungu, iwo ndi okondedwa ake chifukwa cha makolo awo oyambirira.+