Numeri 18:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 “Ndakupatsa iwe zipatso zoyambirira+ za mafuta onse abwino koposa, vinyo yense watsopano wabwino koposa, ndi mbewu zabwino koposa, zimene anthu azizipereka kwa Yehova.+ Miyambo 3:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali+ ndiponso ndi zipatso zako zonse zoyambirira.+ Ezekieli 44:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Zipatso zonse zabwino kwambiri zoyambirira za mtundu uliwonse ndi zopereka zanu zonse za mtundu uliwonse zabwino kwambiri zidzakhala za ansembe.+ Ufa wanu wamisere wochokera ku mbewu zanu zoyambirira muziupereka kwa wansembe+ kuti madalitso abwere panyumba yanu.+ 1 Akorinto 15:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Komabe, Khristu anaukitsidwa kwa akufa,+ n’kukhala chipatso choyambirira+ cha amene akugona mu imfa.+ Yakobo 1:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Pakuti mwa chifuniro+ chake, iye anatibala ife ndi mawu a choonadi.+ Anachita zimenezi kuti tikhale zipatso zoyambirira+ pa zolengedwa zake.
12 “Ndakupatsa iwe zipatso zoyambirira+ za mafuta onse abwino koposa, vinyo yense watsopano wabwino koposa, ndi mbewu zabwino koposa, zimene anthu azizipereka kwa Yehova.+
9 Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali+ ndiponso ndi zipatso zako zonse zoyambirira.+
30 Zipatso zonse zabwino kwambiri zoyambirira za mtundu uliwonse ndi zopereka zanu zonse za mtundu uliwonse zabwino kwambiri zidzakhala za ansembe.+ Ufa wanu wamisere wochokera ku mbewu zanu zoyambirira muziupereka kwa wansembe+ kuti madalitso abwere panyumba yanu.+
20 Komabe, Khristu anaukitsidwa kwa akufa,+ n’kukhala chipatso choyambirira+ cha amene akugona mu imfa.+
18 Pakuti mwa chifuniro+ chake, iye anatibala ife ndi mawu a choonadi.+ Anachita zimenezi kuti tikhale zipatso zoyambirira+ pa zolengedwa zake.