Ekisodo 34:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 “Muzichita chikondwerero cha masabata ndi tirigu woyamba kucha pa nyengo yokolola tiriguyo.+ Muzichitanso chikondwerero cha zokolola kumapeto kwa chaka.+ Levitiko 23:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Muzibweretsa mitanda iwiri ya mkate+ wa m’nyumba mwanu kuti ikhale nsembe yoweyula. Mitandayo izikhala yopangidwa ndi ufa wosalala wokwanira magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Poiphika izikhala ndi chofufumitsa,+ ndipo muziipereka kwa Yehova monga zipatso zoyambirira kucha.+ Chivumbulutso 14:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Awa ndiwo amene sanadziipitse ndi akazi,+ ndipo ali ngati anamwali.+ Amenewa ndiwo amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita.+ Iwowa anagulidwa+ kuchokera mwa anthu, monga zipatso zoyambirira+ zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.
22 “Muzichita chikondwerero cha masabata ndi tirigu woyamba kucha pa nyengo yokolola tiriguyo.+ Muzichitanso chikondwerero cha zokolola kumapeto kwa chaka.+
17 Muzibweretsa mitanda iwiri ya mkate+ wa m’nyumba mwanu kuti ikhale nsembe yoweyula. Mitandayo izikhala yopangidwa ndi ufa wosalala wokwanira magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Poiphika izikhala ndi chofufumitsa,+ ndipo muziipereka kwa Yehova monga zipatso zoyambirira kucha.+
4 Awa ndiwo amene sanadziipitse ndi akazi,+ ndipo ali ngati anamwali.+ Amenewa ndiwo amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita.+ Iwowa anagulidwa+ kuchokera mwa anthu, monga zipatso zoyambirira+ zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.