Genesis 20:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Abulahamu anayankha kuti: “Ndachita zimenezi poganiza kuti, ‘Ndithu anthu a kuno saopa Mulungu,+ andipha ndithu chifukwa cha mkazi wangayu.’+ Genesis 22:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Ndiyeno mngeloyo anapitiriza kulankhula kuti: “Usatambasulire dzanja lako mwanayo ndipo usam’chite kanthu kena kalikonse.+ Tsopano ndadziwa kuti ndiwe woopa Mulungu, pakuti sunakane kupereka kwa ine mwana wako mmodzi yekhayo.”+ Levitiko 25:43 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 43 Musamupondereze ndi kumuchitira nkhanza,+ ndipo muziopa Mulungu wanu.+ 1 Samueli 12:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Koma muziopa+ Yehova ndi kum’tumikira ndi mtima wanu wonse m’choonadi.+ Kumbukirani zinthu zazikulu zimene Yehova wakuchitirani.+ Nehemiya 5:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Ndiyeno ndinati: “Zimene mukuchitazi si zabwino ayi.+ Kodi simuyenera kuyenda moopa+ Mulungu+ kuti tipewe chitonzo+ cha adani athu, anthu a mitundu ina?+ Miyambo 1:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa zinthu.+ Nzeru ndi malangizo zimanyozedwa ndi zitsiru.*+ Miyambo 8:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+ Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso pakamwa ponena zopotoka.+ Machitidwe 9:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Pamenepo mpingo+ mu Yudeya monse, mu Galileya, ndi mu Samariya unalowa m’nyengo yamtendere, ndipo unakhala wolimba. Popeza kuti unali kuyenda moopa Yehova+ ndiponso kulimbikitsidwa ndi mzimu woyera,+ mpingowo unali kukulirakulira.
11 Abulahamu anayankha kuti: “Ndachita zimenezi poganiza kuti, ‘Ndithu anthu a kuno saopa Mulungu,+ andipha ndithu chifukwa cha mkazi wangayu.’+
12 Ndiyeno mngeloyo anapitiriza kulankhula kuti: “Usatambasulire dzanja lako mwanayo ndipo usam’chite kanthu kena kalikonse.+ Tsopano ndadziwa kuti ndiwe woopa Mulungu, pakuti sunakane kupereka kwa ine mwana wako mmodzi yekhayo.”+
24 Koma muziopa+ Yehova ndi kum’tumikira ndi mtima wanu wonse m’choonadi.+ Kumbukirani zinthu zazikulu zimene Yehova wakuchitirani.+
9 Ndiyeno ndinati: “Zimene mukuchitazi si zabwino ayi.+ Kodi simuyenera kuyenda moopa+ Mulungu+ kuti tipewe chitonzo+ cha adani athu, anthu a mitundu ina?+
13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+ Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso pakamwa ponena zopotoka.+
31 Pamenepo mpingo+ mu Yudeya monse, mu Galileya, ndi mu Samariya unalowa m’nyengo yamtendere, ndipo unakhala wolimba. Popeza kuti unali kuyenda moopa Yehova+ ndiponso kulimbikitsidwa ndi mzimu woyera,+ mpingowo unali kukulirakulira.