Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 25:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Musamalandire chiwongoladzanja kwa iye kapena kumukongoza mwa katapira,*+ koma muziopa Mulungu wanu.+ Mnansi wanu ayenera kukhala ndi moyo pakati panu.

  • Nehemiya 5:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Abwanamkubwa amene analipo ine ndisanakhale, ankalemetsa anthu, ndipo tsiku ndi tsiku anali kulandira masekeli* 40 a siliva kuti akagule chakudya ndi vinyo. Komanso atumiki awo anali kupondereza anthu.+ Koma ine sindinachite zimenezo+ chifukwa choopa Mulungu.+

  • Yobu 28:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Ndiyeno anauza munthu kuti,

      ‘Tamvera, kuopa Yehova ndiko nzeru,+

      Ndipo kupatuka pa choipa ndiko kumvetsa zinthu.’”+

  • Miyambo 8:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+ Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso pakamwa ponena zopotoka.+

  • Mlaliki 8:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ngakhale woipa atachita zoipa+ maulendo 100 n’kukhala ndi moyo wautali akuchitabe zofuna zake, ine ndikudziwa kuti anthu amene amaopa Mulungu woona zidzawayendera bwino,+ chifukwa chakuti anali kumuopa.+

  • Malaki 1:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “‘Mwana amalemekeza bambo ake+ ndipo wantchito amalemekeza mbuye wake.+ Ngati ine ndili atate,+ ulemu wanga uli kuti?+ Ngati ndili Ambuye Wamkulu, n’chifukwa chiyani simundiopa?’+ watero Yehova wa makamu kwa inu ansembe amene mukunyoza dzina langa.+

      “‘Inu mukunena kuti: “Kodi dzina lanu talinyoza motani?”’

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena