Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 22:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “Ukabwereketsa ndalama kwa anthu anga, kwa munthu wovutika amene ali pafupi ndi iwe,+ usakhale ngati munthu wopereka ngongole yakatapira* kwa iye. Usafunepo chiwongoladzanja.+

  • Deuteronomo 23:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “M’bale wako usamulipiritse chiwongoladzanja+ pa ndalama, chakudya+ kapena chilichonse chimene munthu angafunepo chiwongoladzanja.

  • Nehemiya 5:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Choncho ndinayamba kuganiza mumtima mwanga ndipo ndinapeza kuti anthu olemekezeka ndi atsogoleri anali olakwa.+ Pamenepo ndinawauza kuti: “Nonsenu mukuumiriza abale anu kukupatsani chiwongoladzanja chokwera kwambiri.”+

      Kenako ndinaitanitsa msonkhano waukulu chifukwa cha iwowa.+

  • Salimo 15:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Sapereka ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja,+

      Ndipo salandira chiphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.+

      Wochita zinthu zimenezi, sadzagwedezeka konse.+

  • Miyambo 28:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Munthu amene amachulukitsa zinthu zamtengo wapatali kuchokera ku chiwongoladzanja ndi katapira,*+ amangosungira zinthuzo munthu amene amakomera mtima anthu onyozeka.+

  • Ezekieli 18:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Iye amakongoza zinthu zake mwa katapira+ ndipo amalandira chiwongoladzanja.+ Ndithudi iye sadzakhala ndi moyo chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi.+ Adzaphedwa ndithu, ndipo magazi ake adzakhala pamutu pake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena