Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 22:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “Ukabwereketsa ndalama kwa anthu anga, kwa munthu wovutika amene ali pafupi ndi iwe,+ usakhale ngati munthu wopereka ngongole yakatapira* kwa iye. Usafunepo chiwongoladzanja.+

  • Levitiko 25:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Musamalandire chiwongoladzanja kwa iye kapena kumukongoza mwa katapira,*+ koma muziopa Mulungu wanu.+ Mnansi wanu ayenera kukhala ndi moyo pakati panu.

  • Nehemiya 5:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndiponso ine, abale anga ndi atumiki anga, tikukongoza ndalama ndi chakudya kwa abale athu. Chonde, tiyeni tileke kulandira chiwongoladzanja tikakongoza zinthu.+

  • Salimo 15:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Sapereka ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja,+

      Ndipo salandira chiphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.+

      Wochita zinthu zimenezi, sadzagwedezeka konse.+

  • Ezekieli 18:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 ngati salandira chiwongoladzanja akabwereketsa zinthu,+ ndiponso sakongoza zinthu mwa katapira,*+ ngati sachita zopanda chilungamo,+ ngati amachita chilungamo chenicheni poweruza munthu ndi mnzake,+

  • Ezekieli 22:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Anthu alandira ziphuphu kuti akhetse magazi.+ Iwe walandira chiwongoladzanja+ ndi kuchita katapira.+ Ukupeza phindu losayenera mwa kubera anzako+ mwachinyengo+ ndipo ine wandiiwala,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena