Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “Usalandire chiphuphu chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu anthu amaso akuthwa, ndipo chingapotoze mawu a anthu olungama.+

  • Deuteronomo 16:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Usamapotoze chiweruzo.+ Usamakondere+ kapena kulandira chiphuphu, chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu maso a anthu anzeru+ ndi kupotoza mawu a anthu olungama.

  • Deuteronomo 27:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “‘Wotembereredwa ndi munthu wolandira chiphuphu kuti akanthe ndi kupheratu munthu, kuti akhetse magazi a munthu wosachimwa.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

  • Salimo 26:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Musachotse moyo wanga pamodzi ndi anthu ochimwa,+

      Kapena pamodzi ndi anthu a mlandu wamagazi.+

  • Yesaya 1:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Akalonga ako ndi aliuma ndipo ndi anzawo a mbala.+ Aliyense wa iwo amakonda ziphuphu+ ndipo amafunafuna mphatso.+ Mwana wamasiye samuweruza mwachilungamo ndipo ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye safuna kuuweruza.+

  • Amosi 5:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Pakuti ndadziwa kuchuluka kwa zochita zanu zondipandukira+ ndiponso kukula kwa machimo anu,+ inu amene mukuchitira nkhanza munthu wolungama,+ amene mukulandira ndalama za chitsekapakamwa+ ndiponso amene mukupondereza anthu osauka+ pachipata cha mzinda.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena