Deuteronomo 15:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 “Wina mwa abale ako akasauka pakati panu, mu umodzi mwa mizinda yanu, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, usamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lako.+ Yesaya 29:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 amene amachimwitsa munthu ndi mawu ake,+ amene amatchera msampha munthu wodzudzula ena pachipata,+ ndiponso amene amagwiritsira ntchito mfundo zopanda umboni pokankhira pambali munthu wolungama.+ Ezekieli 22:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Anthu alandira ziphuphu kuti akhetse magazi.+ Iwe walandira chiwongoladzanja+ ndi kuchita katapira.+ Ukupeza phindu losayenera mwa kubera anzako+ mwachinyengo+ ndipo ine wandiiwala,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Amosi 2:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Iwo akufunitsitsa kuti fumbi la padziko lapansi ligwere pamitu ya anthu wamba+ ndipo sakuchitira chilungamo anthu ofatsa.+ Mwana pamodzi ndi bambo ake akugona ndi mtsikana mmodzi+ ndi cholinga chofuna kuipitsa dzina langa loyera.+ Yakobo 2:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Koma inu simulemekeza munthu wosauka. Kodi si olemera amene amakusautsani+ ndi kukukokerani kumabwalo amilandu?+
7 “Wina mwa abale ako akasauka pakati panu, mu umodzi mwa mizinda yanu, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, usamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lako.+
21 amene amachimwitsa munthu ndi mawu ake,+ amene amatchera msampha munthu wodzudzula ena pachipata,+ ndiponso amene amagwiritsira ntchito mfundo zopanda umboni pokankhira pambali munthu wolungama.+
12 Anthu alandira ziphuphu kuti akhetse magazi.+ Iwe walandira chiwongoladzanja+ ndi kuchita katapira.+ Ukupeza phindu losayenera mwa kubera anzako+ mwachinyengo+ ndipo ine wandiiwala,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
7 Iwo akufunitsitsa kuti fumbi la padziko lapansi ligwere pamitu ya anthu wamba+ ndipo sakuchitira chilungamo anthu ofatsa.+ Mwana pamodzi ndi bambo ake akugona ndi mtsikana mmodzi+ ndi cholinga chofuna kuipitsa dzina langa loyera.+
6 Koma inu simulemekeza munthu wosauka. Kodi si olemera amene amakusautsani+ ndi kukukokerani kumabwalo amilandu?+