11 Munthu wachita zinthu zonyansa ndi mkazi wa mnzake,+ ndipo munthu wachita khalidwe lotayirira mwa kugona ndi mkazi wa mwana wake.+ Munthu wagona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa bambo ake.+
5Mbiri yamvekatu kuti pakuchitika dama*+ pakati panu, ndipo dama lake ndi loti ngakhale anthu a mitundu ina sachita. Akuti mwamuna wina watengana ndi mkazi wa bambo ake.+