Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 35:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Isiraeli atamanga msasa+ m’dziko limenelo, Rubeni anagona ndi Biliha mkazi wamng’ono* wa bambo ake, ndipo Isiraeli anamva zimene zinachitikazo.+

      Yakobo anali ndi ana aamuna 12.

  • Levitiko 20:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Mwamuna wogona ndi mkazi wa bambo ake, wavula* bambo ake.+ Mwamuna ndi mkaziyo aziphedwa ndithu. Mlandu wa magazi awo ukhale wa iwo eni.

  • Deuteronomo 22:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 “Pasapezeke mwamuna aliyense wotenga mkazi wa bambo ake kuopera kuti angavule bambo akewo.+

  • Deuteronomo 27:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi mkazi wa bambo ake, chifukwa wavula bambo akewo.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

  • 2 Samueli 16:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Pamenepo Ahitofeli anauza Abisalomu kuti: “Ugone ndi adzakazi a bambo ako+ amene wawasiya kuti azisamalira nyumba.+ Ukatero Aisiraeli onse adzamva kuti wadzinunkhitsa+ pamaso pa bambo ako,+ ndipo manja+ a anthu onse amene ali ndi iwe adzalimba ndithu.”

  • 1 Akorinto 5:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Mbiri yamvekatu kuti pakuchitika dama*+ pakati panu, ndipo dama lake ndi loti ngakhale anthu a mitundu ina sachita. Akuti mwamuna wina watengana ndi mkazi wa bambo ake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena