Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndipo muyenera kusunga malangizo ndi zigamulo zimenezi, chifukwa mukatero mudzakhala anzeru+ ndi ozindikira+ pamaso pa anthu a mitundu ina amene adzamva za malangizo onsewa. Pamenepo, anthuwo adzanena kuti, ‘Mtundu waukulu umenewu ndi wa anthu anzerudi ndi ozindikira.’+

  • Salimo 111:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova.+

      ש [Sin]

      Onse otsatira malamulo a Mulungu ndi ozindikira.+

      ת [Taw]

      Iye ayenera kutamandidwa mpaka muyaya.+

  • Miyambo 9:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru.+ Kudziwa Woyera Koposa, ndiko kumvetsa zinthu.+

  • Mlaliki 12:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona+ ndi kusunga malamulo ake+ chifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita.

  • Aroma 1:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo,+ makhalidwe a Mulungu osaoneka+ ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha+ ndiponso Umulungu+ wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga+ moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena