Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndipo muyenera kusunga malangizo ndi zigamulo zimenezi, chifukwa mukatero mudzakhala anzeru+ ndi ozindikira+ pamaso pa anthu a mitundu ina amene adzamva za malangizo onsewa. Pamenepo, anthuwo adzanena kuti, ‘Mtundu waukulu umenewu ndi wa anthu anzerudi ndi ozindikira.’+

  • Yobu 28:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Ndiyeno anauza munthu kuti,

      ‘Tamvera, kuopa Yehova ndiko nzeru,+

      Ndipo kupatuka pa choipa ndiko kumvetsa zinthu.’”+

  • Miyambo 1:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa zinthu.+ Nzeru ndi malangizo zimanyozedwa ndi zitsiru.*+

  • Miyambo 9:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru.+ Kudziwa Woyera Koposa, ndiko kumvetsa zinthu.+

  • Mlaliki 12:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona+ ndi kusunga malamulo ake+ chifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita.

  • Aheberi 11:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Mwa chikhulupiriro, Nowa+ atachenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zimene zinali zisanaoneke,+ anasonyeza kuopa Mulungu ndipo anamanga chingalawa+ kuti banja lake lipulumukiremo. Mwa chikhulupiriro chimenecho, anatsutsa dziko,+ ndipo anakhala wolandira cholowa cha chilungamo,+ chimene chimabwera ndi chikhulupiriro.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena