Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndipo muyenera kusunga malangizo ndi zigamulo zimenezi, chifukwa mukatero mudzakhala anzeru+ ndi ozindikira+ pamaso pa anthu a mitundu ina amene adzamva za malangizo onsewa. Pamenepo, anthuwo adzanena kuti, ‘Mtundu waukulu umenewu ndi wa anthu anzerudi ndi ozindikira.’+

  • Yoswa 1:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Buku la malamulo ili lisachoke pakamwa pako,+ uziliwerenga ndi kusinkhasinkha usana ndi usiku, kuti uonetsetse kuti ukutsatira zonse zolembedwamo.+ Pakuti ukatero, udzakhala ndi moyo wopambana, ndipo udzachita zinthu mwanzeru.+

  • 1 Mafumu 2:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Uzimvera Yehova Mulungu wako mwa kuyenda m’njira zake,+ kusunga malamulo ake, zigamulo zake,+ ndi maumboni* ake, malinga ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo cha Mose.+ Uzitero kuti udzakhale wanzeru m’zochita zako zonse, ndiponso kulikonse kumene udzapite.

  • Miyambo 3:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ukachita zimenezi, Mulungu ndi anthu adzakukomera mtima ndipo adzakuona kuti ndiwe wozindikira.+

  • 2 Timoteyo 3:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Kuyambira pamene unali wakhanda,+ wadziwa malemba oyera amene angathe kukupatsa nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke+ kudzera m’chikhulupiriro chokhudza Khristu Yesu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena