20 Tsopano wansembeyo aweyulire zinthuzo uku ndi uku monga nsembe yoweyula kwa Yehova.+ Zinthuzi zipite kwa wansembeyo ngati mphatso yopatulika, limodzi ndi nganga+ ya nsembe yoweyulayo, komanso mwendo umene aupatula kuti ukhale chopereka.+ Pambuyo pake yemwe anali Mnaziriyo angathe kumwa vinyo.+